02/08/17

Written by  Newsroom

Banja lina liweyeseka ku Machinga
Banja lina pa mudzi wa Kumbalangwe kwa Nkula m’boma la Machinga laweyeseka.

02
August

Nkhaniyi ikuti mkamwini wina anakwatira pa mudzipo kuchokera kwao ndipo amakhala ku chikamwini. Mkammwiniyo wakhala akuuza mkazi wake kuti azimuwambira mbewa ku mpani ngakhale kuti mkaziyo komanso achibale ake samadya mbewa. Ngakhale mkaziyo wakhala akukana kumphikira mbewa mwamuna wakeyo. Koma pakutha kwa miyezi pang’ongono ndi pang’ono mkaziyo anayamba kufookera ku zofuna za mwamuna wakeyo. Makolo atazindikira za nkhaniyi anayamba kumasala banjalo mpaka wosamwapo ngakhale madzi. Makolowo anafika polangiza mwana waoyo kuti athetse banjalo koma mtsikanayo akukakamira. Pakadalipano mkamwiniyo akuganiza zothawitsana ndi mkazi wakeyo kuti azikakhala m’dera lina. Koma mphekeserayo itawapeza makolo anenetsa kuti ngati amutsatire mwamunayo ndiye kuti sakhalanso mwana wao.

 

Mayi wina athawa ana ake

Tili m’boma la Machinga lomwelo koma mdera la Ngokwe ana amai wina azingwa, mai wao atawathawa. Nkhaniyi ikuti maiyo yemwe ndi wokonda kupapira bibida ali ndi banja lake lodziwika bwino mderalo. Koma kamba koti amakonda kupapira kabanga masiku apitawo anapita pamudzi wina mderalo kuti akazipepese pokumwa mowa wachilendo. Ndipo izi zinathekadi. Ali mkati mopapila kabangayo pamalopo panafika njonda ina yomwe siphethira diso ikaona siketi. Ndipo limodzi ndi abambo ena omwe analinso pamalopo anayamba kugula mowa mwakathithi pofuna kukopa mkaziyo. Ndipo njondayo inakwanitsa kutenga maiyo kuyamba kunong’onezana nkhani zonsamveka bwino. Mosakhalitsa awiriwo anasowa pamaolo koma nkuti nthawiyo atatapatika. Koma patapita nthawi mwini malowo anadabwa kupeza anthu awiriwo ali mbulanda mkitchini yake komanso ali mtulo tofa nato. Apo sanachedwe koma kuitana anthu ena kudzamuonesa malozawo. Mai wamunchunuyo atadzikndikira kuti madzi achita katondo anavumbuluka pamalopo ngati kalulu wopulumuka ku moto wolusa. Mpaka lero maiyo sakudziwika komwe ali zomwe zachititsa kuti ana ake awiri kudzanso zizukulu zili azikhala okha opanda kholo.

 

Mkulu wina athamangitsidwa kamba kochita za matsenga

Bambo wina mdera la Kapichi m'boma la Thyolo amuthamangitsa pa mudzipo  kamba koti amachita zamatsenga. Nkhaniyi ikuti mkuluyu adakonza upo ofuna kupha mwa matsenga bambo wina yemwe amapanga rent nyumba yake. Masiku apitawo mkuluyu anapita kwa msing'anga komwe anakatenga mtela kuti aphe bambo wa rent-yo. Koma zinakanika kamba koti nayenso anazama pa zitsamba. Zomwe zinachititsa kuti mwini maloyo apenge mpaka kuyaluka poulula zachipongwe zomwe amafuna kuchitra walendi wakeyo. Koma wa renti-yo atafunsa anthu ena zoti achite iwo alangiza kuti angochoka mderalo. Ndipo anthu ena okhala mderalo kamba kokwiya ndi mwini maloyo alandula kuti achoke mderalo ndipo akapanda kutero amutengera kubwalo kamba ka nkhani za ufiti komanso matsenga. Pakadali pano mkuluyo akuganiza zosamukira dera lina poopa zomwe alonjeza anthu okwiyawo.

 

Adulilidwa njinga ndi mwini mkazi

Mwamuna wina manja ali nkhosi kwa Gulupu Likoto mdera la M’bisa m’boma la Zomba mwini mkazi yemwe anali naye pa ubwenzi wamseli atadula njinga yake zidutsa-zidutsa. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mderalo muli njonda ina yomwe masiku apitawo inathetsa banja lake ndi mkazi wina ngakhale ali naye ana. Apo njondayo inakwatira mkazi wina, nayenzo mkazi wake wakaleyo anapeza mwamuna wina yemwe wamanga naye banja. Koma zomwe zakhala zikudabwitsa anthu kumene ndi zooti awiriwo anaymba kuzemberananso. Ngakhale mwamuna watsopanoyo adafunso mkazi wakeyo iye adakanitsitsa kwamtu wagalu kuti ndi nkhamba kamwa chabe. Koma masiku apitawo madzulo atsiku lina mkaziyo analawira mwamuna watsopanoyo kuti akupita kuchitsime kukatunga madzi. Chonsecho akukakomanda ndi mwamuna wake wakele uja. Koma momwe amachoka pakhomo mwini mkaziyo sanakhutire ndi zomwe mkaziyo amachita. Apo anayamba kumtsatira mpaka kumpeza ali ndi mwamuna wake wakale uja atayala nsalu pansi pamtengo wina koma njinga yake ili potero. Apo mwini mkaziyo yemwe anali ndi nkhwangwa mmanja mwake sanachitire mwina koma kukhapa njingayo mpaka kuisiya ili tidzidutswa tokha-tokha. Pakadali pano mwini njingayo wasowa pogwira kamba ntchito yakabanza yomwe amachita yaima tsopano.

Get Your Newsletter