01/08/17

Written by  Newsroom

Mwini mbumba adabwitsa anthu
Tili m’dera la mfumu Chimaliro m’boma la Thyolo, mwini mbumba wina wadabwitsa anthu kumeneko.

01
August

Nkhaniyi ikuti masiku apitawa mai wina anapeza mwamuna woti amange naye banja. Nkhani yokondweretsayi itafika pamudzi, anthu anasankha mkulu wina kuti ndiye akhale nkhoswe yakuchikazi kamba koti ngwa makhalidwe abwino. Izi zinachitikadi ndipo mwambo wonse wachinkhoswe unayenda bwino. Koma ngakhale zonse zinayenda bwino chomwechi panalibe yemwe amaganiza kuti awiriwo ali pa ubwenzi. Patangodutsa sabata imodzi chichitire mwambo wachinkhoswewo, ankhoswe akuchikaziwo apezeka pamalo ena ogona anthu apa ulendo m’boma la Thyolo ali mchikondi ndi mai yemwe anamugwirizira unkhosweyo. Pakadali pano anthu ena akuganiza kuti mwina anthu awiriwo akhala ali pa ubwenzi wamseli kuchokera pakanthawi. Nkhaniyi yagwedeza banja latsopanolo ndipo awiriwo akuyenda njira zachidule chifukwa cha manyazi.


Mayi wina agona ngati wafa
Mayi wina ku Ekwendeni mboma la Mzimba wadabwitsa anthu atagona tulo tofa nato mpaka osamva kulira kwa mwana wake wa miyezi isanu ndi umodzi. Nkhaniyi ikuti mwamuna wa mayiyo amachita bizinesi ya Barber shop pa sitolo zina m’deralo ndipo akachoka m’mawa amafika pakhomo madzulo. Patsikulo mayiyo atangodya nkhomaliro cham’ma 12 koloko masana, anaganiza zophwetsa nkhuto ndipo anakagona m’nyumba mpaka kudzitsekera kuchipinda. Yemwe watumiza nkhaniyi wati anthu oyandikana naye nyumba anadabwa kumva kulira kwa mwana m’nyumbamo mosonyeza kuti alimo yekhayekha. Anthuwo anayesetsa kuitana mokuwa maiyo koma sanayankhe ndipo atayesa kutsegula chitseko anapeza chokhoma zomwe zinawalepheretsa kupulumutsa mwanayo. Chomwe chadabwitsa anthuwo nchoti mayiyo anadzuka cham’ma 7 koloko madzulo, pomwe mwamuna wake amafika pakhomopo kuchokera ku bizinesi yakeyo. Anthuwo ati mpaka pano sakumvetsa chomwe chinachitika kwa mayiyo ngakhale mwamuna wakeyo sanayankhulepo kanthu pa nkhaniyi. 

 

Mwana wina amenyedwa kamba koyenda ndi a phunzitsi
Ophunzira wina wa mkazi m’boma la Nsanje yemwe ali form 3 pa sukulu ya sekondale yogonera konko wamenyedwa kodetsa nkhawa kamba koyenda ndi Mphunzitsi wake wa pa sukulupo. Mtsikanyo ndi chiphadzuwa ndipo wakhala akuzemberana ni mphunzitsiyo yemwe ali pa banja. Atsikana ena anatsina khutu mwini mwamunayo yemwenso ndi mphunzitsio wa mkazi pa sukulupu za nkhaniyi. Kenaka mwini mwamunayo anapita kumalo ogona atsikanawo ku Ma Hostel ndikamududuliza mtsikanayo uku akumutibula mwankhanza. Mwini mwamunayo akuti anamuponyera zibagela zoonetsa nyenyezi usana mpaka kumung’ambila zovala zake ndikumusiya ali thapsya. Ndeu-wu inasowa oleletsa kamba koti mtsikanayo amalankhula mwathamo kuti palibe angawopsyeze ndipo iye salekana ndi mphunzitsiyo. Pakadali pano nkhaniyi yawapeza akulu akulu amaphunziro m’bomalo omwe akukonza zopanga chiganizo pa nkhaniyi ndipo zikumveka kuti mwina banjalo alitsamutsa pa sukulupo

 

Mnyamata wina awophyeza anthu kuti awalodza

Mnyamata wina wopempha-pempha mu mzinda wa Blantyre akuti akuopsyeza anthu ena kuti awaloza ngati samumupasa zomwe akufuna. Mnyamatayo akuti amakhala ku mbayani ndipo amayenda m’makhomo mwa anthu kupempha zakudya ndi ndalama. Koma zokhumudwitsa ndi zoti akafika pakhomo ndikupeza kuti mwini khomolo alikwakwa Mnyamatayo amanyoza ndikuopsyeza kuti awaloza anthuwo komanso akapeza kuti pakhomopo palibe anthu, mnyamatayo amatha kulowa mnyumba ndikuba zithu mkuthawa. Anthu ena ati ndi okhumudwa kuti nthawi zina mnyamatayo amamupeza ali zandi-zandi pa mowa ataledzera moiwala kwao ndikumalankhula mothumbwa kuti ndi olemera kwambiri. Pakadali pano anthuwo achenjeza kuti akamutula mnyamatayo m’manja mwa achitetezo akapitiliza khalidwe lakelo.

Get Your Newsletter