28/07/17

Written by  Newsroom

Athamangitsa mayi ake kamba ka malo

Mikoko yogona ku Manyowe m’boma la Blantyre yapukusa mitu kamba ka zomwe akuchita nmyamata wina pothamangiza mai ake kamba ka malo.

28
July

Nkhaniyi ikuti bamboo wina anakwatila mai wina ndipo anakhala pa banja zaka zambiri. Mwatsoka bamboyo amadwala mpaka kuthiphwa mkumwalira. Mwambo wa maliro utatha ndipo siku losesa maiyo anakoma mtima poitana ana ena omwe amalemuyo anabereka ndi mai wina woyamba ndicholinga choti azikhala limodzi pamudzipo. Kenaka m’modzi mwa mwana wa mamuna wa malemuyo anasintha manga mkuyamba kucghitila khanza maiyo . Mnyamatayo akuti akumalandila ndalama za Rent za nyumba zonse ndkulakhula mwathamo kuti mai akewo akangoyelekeza kulandila ndalamazo awona zakuda. Ngakhale akulu akulu odziwa za milandu akhala akudzudzula mnyamatayo iye wamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti zivute zitani mai ake-wo asamuka pa malopo ndipo adzipita kwawo ku Khwisa ku Balaka. Anthu ambiri akuti ndi okhumudwa kamba koti Mai-yo wakhala ndi Malemu mwamuna-yo kwa zaka makumi anai ndipo akudela nkhawa kuti akafikila kuti. Pakadali pano Nyakwawa ya mderalo yaoopsyeza kuti ithana ndi mnyamatayo ngati apitiliza maganizo ake olanda malo-wo kwa mai-yo.

 

Njonda ina itibulidwa 

Paja akulu-akulu adati atambwali sametana , izi zapherezera m’mudzi wa Chikowi m’boma la zomba komwe Njonda ina ya Chitetezo cha m’midzi ayitibula mpaka thapsya . Chomwe chachitika nchoti amuna awiri omwe ndi oyandikana nyumba analowa mgulu loyang’anila za chitetezo cha m’midzi . Koma tsiku lina mzakeyo ali kogulitsa malonda njonda inayo inazemba ndikukalowa kumpanda kwa mzake wa chitetezoyo ndikuba nkhuku. Koma mphuno salota potuluka njondayo inangoti gululu ndi mwini nyumbayo. Kenaka anamuphaphalitsa mafunso koma anangoti ndwi osankha . Apa mkuluyu anangotenga ndodo ndi kuwumbuza mzakeyo mpaka anagwa pansi. Koma ataona kuti madzi achita katondo njondayo iandzuka mkuthawa.Pamene mkuluyu amafika pa malopo mkuti mwamunayo ataliyatsa liwilo la m tondo wa dooka. Koma mkuluyu atazindikila kuti ayitulukila m’mawa kutacha mkuluyu anathawa ndipo sakudziwika komwe apita ngakhale zikumveka kuti mkuluyu wathawila kwa Mayaka m’bomalo.

 


Azimjayi awiri akanganilana chuma cha mamuna odwala 

Amai ena awiri ku Chipatala cha gulupu mu mzinda wa Blantyre akangana koopsya chifukwa chokanganila chuma cha mwamuna wake yemwe akudwala. Chomwe chachitika mchoti mwamuna wina amadwala ndipo anamugoneka pa chipatala-cho. Mkuluyu ndi mponda matiki ndipo ali ndi akazi awiri. Koma chomwe chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga mchoti nthawi zonse pamene mwamunayo akamadwala m’modzi mwa amaiwo ndi amene akhala akumusamala mwamunayo ndipo atayamba kupeza bwino, achipatala anamutulutsa kuti adzikalandila nthandizo ku nyumba. Koma anthu anangoti kakasi m’modzi mwa mkazi wa mwamunayo atabisa makiyi ndipo mkangano unabuka. Akazi awiriwo anayamba kukangana uku akukokelana kuti mwamunayo akagone ku nyumba kwake. Izi zinakwiyitsa odwalayo ndipo anakagona pansi pa mtengo ndikusiya amai awiriwo akukangana . Anthu omwe amaona izi zikuchita ati sakudabwa kamba koti amai-wo akukangana kamba ka chuma osati kuchitila chisoni mwamuna wakeyo.

Mwambo wa ukwati usokonekela

Mwambo wa ukwati kwa Kachere m’boma la Dedza unasokonekera aku chimuna atapeza kachingwe ka Neckless nkhosi mwa nkhuku yemwe anapha pa ukwatipo. Chomwe chachitika mchoti mwamunayo anakwatila mtsikana wina ndipo tsiku laukwati zonse zimayenda bwino. Koma nthu anakhumudwa atapeza nkhosi mwa nkhuku ina yomwe anapha ndipo pososola nkhosi mwake munali Neckless yolembedwa kuti mkaziyo ndi wanga. Pamenepa anthu anayamba kukambilana kuti apeze munthu yemwe wachita za malozazo. Kenaka munthu wina anaulula kuti munthu wina yemwe sakuziwika anapereka nkhukuyo madzulo ngati mphatso ndipo anasowa pa malopo. Anthu ena akuganiza kuti mwamuna wina yemwe amafuna kumukwatila mkaziyo ndi amene anabweretsa nkhukuyo ndi cholinga choti mwamunayo akwiye ndi kunyanyala mwambowo. Pakadali pano mwamunayo wanenetsa kuti samusiya mkaziyo ndipo apempha akulu akulu a mpingo kuti alowelere pa nkhaniyi kamba koti mwina akuganiza kuti zamasenga zikuchitika m’banjamo.

Get Your Newsletter