27/07/17

Written by  Newsroom

Banja litha atamenya mamuna kumalo obisika
Mai wina ku Zalewa manja ali ku nkhongo kamba koti banja lake latha atamenya mwamuna wake ku malo obisika.

27
July

Nkhaniyi ikuti mai-yo wakhala pa banja ndi mwamunayo kwa zaka zambiri mpaka kukhala ndi ana anai . Koma chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga mchoti mwamunayo amagwira ntchito ku kampani ina mderalo ndipo pa zifukwa zina ntchito-yo inatha. Pamenepa mai-yo anayamba kulalatila mwamunayo kuti akungokhala manja lende. Kenaka mai-yo ananamiza mwamuna wake-yo kuti adzichita bizinesi yogulitsa mondokwa. Poyambilira zinthu zimayenda bwino koma kenaka mkaziyo analowerela mpaka kumabwera mochedwa pakhomopo. Zikumveka kuti nthawi zina amagona komwe anapita kukatenga katunduyo zomwe zinzchititsa mwamunayo kukayikila ndi khalidwe la mkaziyo. Tsiku lina mkaziyo anatenga ndi mwamuna wina ndikukagona ku malo ogona alendo ndipo m’mene amachita izi mkuti anthu ena akumuona. Anthuwo anatsina khutu mwamuna wake ndipo atafika kumaloko sanakhulupilire atamupeza mkazi wakeyo atakolekana miyendo ndi mwamuna wakubayo. Pamenepa mwamuna wakeyo anangofikila kumenya mwamunayo ndipo mkaziyo anathawa . Koma atafika ku nyumba mkaziyo anayamba kulalata uku akunenana motumbwa kuti mwamunayo amamusatasata kamba ka nsanje ndi anamugwira ndi ku mucheka malo obisika ndipo anagwa pansi. Anthu ena anatengela mwamunayo ku chipatala china komwe akulandila thandizo. Pakadali pano mwamunayo walamula mkaziyo kuti achoke pa khomopo kutathandauza kuti banja latha. Anthu ambiri akumuseka mkaziyo kamba kopasula banja lake chifukwa chokonda ndalama.

 

Alandidwa maliro

Ana a banja lina m’boma la Thyolo manja ali ku nkhongo atawalanda maliro a bambo awo pa chipatala china m’boma la Blantyre. Chomwe chachitika mchoti bamboyo anali pa banja ndi mai wina ndipo mulungu anawadalitsa mpaka kukhala ndi ana ambiri . Mwatsoka bamboyo anayamba kudwala mpaka kuthipwa ndipo anamugoneka pa chipatala china mu mzinda wa Blantyre. Matenda anakula mpaka bamboyo anamwalira. Pamenepa anawo anatumiza uthenga wa imfayo kumudzi kwawo ndipo anthu anakhala thcelu pofuna kulandila malirowo. Koma mwadzidzidzi ku chipatalako kunatulukila achibale a mwamunayo omwe anauza anawo kuti Malemuwo apita nao kwawo ku Ntcheu. Chiphwilikiti chinabuka ndipo anthuwo sanagwirizane kufikila anthuwo ananyengerela dalaivala yemwe ananyamula thupi la malemuyo ndikukabisala kwa Kameza. Pamenepa ena mbumba anangobalalika pa malopo. Kenaka m’modzi mwa anawo anapita kukaona komwe inayima galimoto yomwe munali thuphi la bamboo ake koma sanaipeze. Atasatila anapeza kuti aku chimunawo anali atathawitsa malilowo kupita nao ku Ntcheu. Pakadali pano ana a malemu-yo ati ndi okhumudwa ndi zomwe achita achibalewo kamba koti nthawi yomwe malemuwo amadwala iwo samazonda matendawo.

 

Nyakwawa inyanyalidwa maliro
Tili pa nkhani ngati yomweyi Nyakwawa ina ayinyanyalila maliro ku Soche m’boma la Blantyre. Chomwe chinachitika mchoti mwamuna wina amadwala mpaka kuthipwa mpaka kumwalira. Malemu-yu anamanga nyumba yake m’mudzimo ndipo wakhala zaka makumi atatu. Mkuluyu anawuza ana ake, akulu akulu a mpingo ndi nyakwawa ya m’mudzimo kuti akadzagonela mkpnp adzamuyike mderalo. Koma chokhumudwitsa mchoti mkuluyu atamwalira achibale anafika kuchokera ku Mulanje stsnysmuls chitantha kuti adzanyamule thupi la malemuwo. Koma anthu pasiwapo anamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti anthuwo awona zakuda ngati angapitilize maganizo oterewo. Pamenepa achibalewo ananyanyala pasiwapo ndikusiya mwambo onse m’manja mwa nyakwawayo. Pakadali pano mwambo wa maliro wachitika motsogozana ndi ndi nyakwawayo. Anthu ena ati ndi okhumudwa ndi zomwe achita achibalewo pokana kuyendetsa nao mwambowo.

 

Akunthidwa kamba kokuba nyama
Mkulu wina wochita malonda pa sitolo zapa Kalolo m’boma la Lilongwe amutibula mpaka thapsya kamba kakuba nyama. Chomwe chachitika mchoti m’modzi mwa mai wina yemwe amachita malonda pa sitolozo amadwala mpaka kumwalira . Akulu akulu a mpingo anayendetsa mwambowo mpaka unayenda bwino mpaka kumanda. Koma munthu wina yemwe ndi otchuka kwambiri anatuluka ku mandako mofulumila ndikukalowa mnyumba ina momwe munali chakudya pa siwapo ndikukhutula ndi zonse zomwe zinali mu mphika wina ndikuthira m’jumbo. Koma pa nthawi yomwe amatuluka mnyumbamo anangoti gululu ndi m’modzi mwa anafedwa yemwe anaphaphalitsa mafunso mkuluyu koma anangoti zoli kusowa choyankha ndipo m’modzi mwa anafedwawo anakuwa ndipo anthu onse omwe amachokera ku mandako anakhamukira ku nyumbako komwe anapeza mkulu wakubayo . Apa anthuwo anamutibula mkuluyo mpaka magazi kukamwa uku akupepesa kuti analibe ndiwo ku nyumba kwake. Pakadali pano nyakwawa ya m’mudzimo amulipilitsa mbudzi ziwiri kamba kakhalidwe lake loipa.

 

Get Your Newsletter