26/07/17

Written by  Newsroom

Mkulu wina yemwe ndi msodzi ku Lumbaulu m’dziko la Mozambiki waopsyeza kuti athana ndi munthu aliyense yemwe wamudyera nsima yake ya ndiwo nsomba.

26
July

Nkhaniyi ikuti mkuluyo ndi msodzi ndipo ku nyanjako anamangako chisakasa malinga nkuti nthawi zambili amakhala kumeneko. Patsikulo mkuluyo anagula nsomba ya mlamba yomwe anachalira kuti adyere mgonero ndipo anakapereka ku nyumba kuti mkazi wake amukonzere. Mkaziyo anaphikadi bwino ndiwoyo ndipo kenaka anaphika nsima nkumupatsira mwana kuti akawapatsire atate ake ku nyanjako. Kumeneko mwanayo anakapeza atate akewo kulibe, atapita ku Nyanja kukaweza usipa ndipo apa anangosiya nsimayo pa khonde iye nkumapita. Mwanayotu anachita izi monga momwe amachitira masiku onse. M’mbuyomu anyamata ena omwe sakudziwika akuti anakwekweza nsima ya nsombayo nkudya ndipo m’mene amabwera mkuluyo anapeza mbale zokha. Atafunsa anthu ena oyandikira pamalopo, anati sanaone yemwe wadya nsimayo ndipo izi zinakwiyitsa kwambili mkuluyo mpaka waopsyeza kuti athana ndi aliyense yemwe akukhudzidwa ndi chipongwecho.


Mayi wina wa m’mudzi mwa Maganiza m’dera la Mfumu Mkanda mboma la Mulanje waimika manja m’mwamba kuti ukwati waulephera, mwamuna wake atayamba kumukakamiza kuti azisewera ku chipinda pamene mayiyo ali ndi mwana wa khanda. Nkhaniyi ikuti mayiyo wangobadwitsa kumene mwana wa khanda yemwe panopa wangotha sabata ziwiri zokha. Tsono chomwe chautsa mapiri pa chigwa nchoti mwamuna wake m’nyumbamo anayamba kuvuta kuti ayambe kukhala malo amodzi koma mayiyo anakanitsitsa kwa ntuwa galu. Popsya mtima, mwamunayo akuti anamenya mkazi wakeyo zomwe zinachititsa kuti mayiyo akadandaule kwa akuluakulu ena pamudzipo. Ku bwalolo mayiyo nkhani inamugomera chifukwa choti ati akuluakuluwo anamulangiza mayiyo kuti asamamukane mwamuna wakeyo ku chipinda poopa kuti atuluka kunja kukafuna akazi ena. Chigamulochi sichinasangalatse mayiyo moti panopa wamenyetsa nkhwangawa pa mwala ponena kuti sangalole zomwe akufuna mwamuna wakeyo ndipo wati akapitiliza kumuvutitsa ku chipinda panopa, alolera kuti banjalo lingotha. M’mene timalandira nkhaniyi nkuti banjalo likupitilirabe ndipo ambili ali nchikhulupiliro choti anthu awiriwo amvana chimodzi pa nkhaniyi.


M’dera lomwelo la Mfumu Mkanda, mkamwini wina wamenyana ndi apongzi ake chifukwa chotukwana ndi kumulalatira. Nkhaniyi ikuti mkamwiniyo patsikulo anagula za nkhuli ku nyumba kwake koma vuto nloti apongozi ake sanawagulire zawo kapena kuwagawirako. Izi zinakwiyitsa apongozi akewo mpaka anayamba kumulalatira kwinaku akumutukwana zamu nsalu. Popsya mtima, mkamwiniyo anagwira apongozi akewo nkuyamba kuwakuntha. Ndeuyo inakula chifukwa nawo apongoziwo analimba nazo zibakera. Nkhaniyi inakafika ku bwalo la Mfumu komwe mkamwiniyo walandula kuti sangasekerere khalidwe la apongozi akewo ndipo wati akangokolola chimanga chomwe walima pamudzipo adzipita kwawo. Paza banja ndi mkazi wake, mkamwiniyo wati alibe chifukwa ndi mkaziyo ndipo ngati akumufunabe amutsatira kwawo komwe adzikakhala ngati mtengwa. Pakadali pano anthu ambili m’mudzimo adzudzula mayiyo chifukwa chofuna kusokoneza banja la mwana.


Mayi wina wa m’mudzi mwa Msaiwa kwa T/A Kaduya ku Migowi mboma la Phalombe wayaluka atamupezelera akuchita za dama ndi njonda ina m’nyumba. Nkhaniyi ikuti mayiyo mwamuna wake amagulitsa makala ndipo nthawi zambili amakaswera ku tchire komwe amakaotcha makalawo. Patsikulo mwamunayo atabwera kutchireko, anakagona ku chipinda kuti apumule. Koma m’malo moti mayiyo akhazikike pakhomopo anaganiza zokakumana ndi chibwenzi chake m’mudzi momwemo. Mwamunayo atadzuka anapeza mkaziyo palibe ndipo atamuyimbila foni anamuyankha kuti ali kwa mayi ake. Mwamunayo analondola kwa apongozi akewo koma zachisoni kuti sanakampeze ndipo atamuimbiranso foni anamuyankha kuti ali kwa nzake wina m’mudzi momwemo. Apatu mwamunayo anadziwa kuti mkaziyo akumuyimba ndipo apa anangolondola kwa chibwenzi chakecho malinga nkuti anayamba kale kuwakayikira. Atafika kumeneko anaimbanso foni ndipo anamumva akuyankha m’nyumba ya njondayo. Apatu mwamunayo anangogwejula chitseko nkulowa ndipo apa anayamba kuwathidzimula onse awiri. Pa ndeuyo mwini mkaziyo akuti anavulaza anthuwo mpaka anakamutsekera m’chitokosi cha apolisi. Pakadali pano mkuluyo watuluka m’chitokosimo koma nzokaikitsa ngati banjalo lipitilire ndi mkazi wachimasomasoyo.

Get Your Newsletter