14/07/17

Written by  Newsroom

Mwamuna wa bizinesi abindikila mnyumba
Mwamuna wina wochita bizinezi ya golosale ku Chikangawa m’boma la Mzimba akukhalira kubindikira nyumba chifukwa cha manyazi.

14
July

Mkazi wa mwamunayo wakhala akudzudzula paza khalidwe la nchuuno la mwamuna wakeyo koma iye amakanitsitsa paza mphekeserayo. Miyezi ingapo yapitayi njondayo inapalana ubwenzi wa mtseri ndi mtsikana wina wachichepere ndipo mkazi wa mwamunayo anazindikira za ubwenziwo. Koma pofuna kusungilana ulemu mkaziyo samamufunsa mwamunayo ponena kuti adzagwira yekha. Masiku apitawa mwamunayo anapangana ndi njoleyo kuti akakumane pa malo ena ndipo izi zinachitikadi koma osadziwa kuti anthu ena anawaona. Anthuwo pokwiya ndi zomwe njondayo yakhala ikuchita mderalo anakauza mkaze wake za nkhaniyi. Apa mkaziyo pamodzi ndi anthuwo anatsagana kuti akaone za malodzazo. Atafika pa tchirepo anapeza mkuluyo ndi mtsikanayo ali buno bwamuswe ndipo anthuwo kunali kumenya kosawamvera chisoni mpaka mwamunayo zinankoka manja mpaka kulephera kuthawa. Mwamunayo anachonderela anthuwo kuti awasiye koma m’malo mwake anangowalora kuti avale zovala zao ndikuwakokera ku bwalo la Nyakawawa. Ku bwaloko njondayo ndi mtsikanayo anavomereza za kulakwa kwao zomwe zinapangitsa kuti awakhululukire koma anawalipitsa chindapusa cha 10-thousand kwacha. Pakadali pano mwamunayo ndi mtsikanayo akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha nmanyazi, koma banja la njondayo laweyeseka.

Mayi wina adzudzulidwa
Anthu ena kwa gulupu Khoswe m’boma la Balaka adzudzula kwambiri mai wina pa zomwe wachita. Maiyo wakhala pa banja ndi mphongo ina yomwe imagaisa mchigayo mpakana kumangira nyumba ya malata maiyo. Miyezi ingapo yapitayi maiyo poona kuti zake zamuyendera anagwirizana ndi abale ake kuti athamangitse mkamwiniyo pa khomopo mu njira yomusemera chinyau. Nkhaniyi ikuti akuchikazi anayamba kupezera zifukwa mwamunayo mcholinga choti akawawidwa mtima achoke yekha pakhomopo zomwe mwanmunayo anazitulukira. Mwa zina akhala akumuloza chala kuti amachita zamatsenga komanso kusokoneza mabanja a weni zomwe anthu ambiri mderalo sakugwirizana nazo. Pa chifukwachi azilongo a maiyo amakhalira kulankhula zachipongwe mkamwiniyo akaledzera kabanga mpakana kumutukwana pa zifukwa zosadziwika bwino. Mkamwiniyo poopa kuti adzangofera za eni anatsanzika pakhomopo koma akudandaula kwambiri kuti anavutika kuomba njerwa ndikumangira mkaziyo mnyumba yabwino kwambiri. Aku chimuna nawo ati sasiila pomwepa koma kukatula nkhaniyi ku bwalo kuti bwalolo ndilo linga gamule. Chimene akufuna akuchimuna nkuti ngati kuli kotheka bwalolo ligulitse nyumbayo kuti waoyo aone polilira pambuyo pogawana ndalama.

Mnyamata wina aseketsa anthu
Mnyamata wina yemwe amaoneka kuti mutu wake suyenda bwino anaseketsa anthu kwa Malirana ku Dedza. Mnyamatayao ngakhale mutu wake sumayenda bwino ngodzidalira kudzera pa ntchito yaulimi ndi zina. Mwa zina mnyamatayo amakhala pamudzi pa makolo ake koma ali ndi nyumba yake komanso amadzipezera yekha chakudya ndi zina zonse pa umoyo wake. Kwa nthawi yayitali anthu akafuna kuti alowe nmnyumba mwake amawazazaila ponena kuti mnyumbamo muli katundu wake ndipo izi zakhala zikudabwitsa anthu pamudzipo. Masiku apitawa mderalo munachitika zovuta ndipo mnyamatayo anatulutsa mutu wa gule wotchedwa SAJENI omwe iye anauumba bwino lomwe. Mnyamatayo anasenza katundu wakeyo pamutu uku akuvina kupita naye ku maliro kuja. Apa anthu omwe anali pa siwapo anali ozizwa pamene akuluakulu aku dambwe zinawaipila kwambiri. Koma ngakhale anthuwo zinawaipila anthu omwe anasonkhana pa maliropo anaseka chikhakhali mpakana mwambo wa maliro unasokonezeka kwa nthawi yayitali. Pamene timalandila nkhaniyi mikoko yogona komanso akuluakulu a dambwe akhalirana pansi kuti aone chochita koma Nyakwawa ya mderalo yati palibe chomwe angachite ndi nkhaniyi chifukwa munthuyo mutu wake sugwira.

Get Your Newsletter