13/07/17

Written by  Newsroom

Athawa kuntchito kamba ka ngongole

Mkulu wina wathawa ku ntchito kwake chifukwa cha ngongole mdera la Kapoka m’boma la Chitipa.

13
July

Yemwe watumiza nkhaniyi wati kumeneko kunali mkulu wina yemwe kwawo ndi m’boma la Machinga ndipo amagwira ntchito mdera la Kapokalo. Koma ndalama zomwe ankapeza sizimakwanila iye anayamba moyo wotenga ngongole kwa anzake. Kamba iye samaopa kubwereka ndalamazo ngongoleyo zinachulka mpaka kulephera kubweza. Ndipo eni ndalamazo anayamba kuvutitsa nkuluyo kuti abweze koma iye ankangozengeleza. Tsono tsiku lina anangoti gululu ndi ena mwa eni ndalamazo omwe amaoneka olusa kwambiri. Maso awo ali ofiili ngati awathira tsabola anakwenya nkuluyo kuti apereke ndalamazo. Apo kathyaliyo anawabwatika anzakewo kuti amudikire pomwe anakomanapo ndipo akupita kunyumba kwake kotenga ndalamazo. Apo njondayo italowa mnyumbayo inapakila katundu wake ndikutulukira khomo lakuseri. Anthuwo anadabwa kuona kuti munthuyo sakubwera kuzapereka ndalamazo. Anthu atakafunsa kwa alandlord a njondayo, iyo adayankha kuti mwina wapita kumtsinje kuchapo zovala zake, konseko kuli kuwabwatikanso anthuwo. Pakadali pano zamveka njondayo yasamukira mu mzinda wa Mzuzu.

 


Atuwisidwa ndi zibagela 
Anthu anafa ndi phwete kwa gulupu a Chauma mdera la mfumu Malili m’boma la Lilongwe, mnyamata wa zaka 17 atatuwitsa ndi zibakera bambo wina wa zaka zoposa makumi anai. Yemwe wakhala akutsata bwino nkhaniyi wati mderalo muli mkulu wina yemwe ngwa matama kuti amtha kumenya kwambiri. Ndipo zaka zapitazo m’ng’ono wake wa mkuluyo anapeza mkazi woti amange naye banja. Koma pa zifukwa zina ubwenziwo sunapitlire. Maka poti mtsikanayo ngomatsuka, iye anayambanos kumacheza ndi anthu osiyana-siyana mderalo kuphatikizapo anyamata. Ndipo tsiku lina mkulu wa thamoyo adapeza mtsikanayo akucheza ndi mnyamata wina mderalo. Kamba ka msanje kuti mtsikanayo anali mkazi wa mng’ono wake iye anaymba kulalatira mnyamatayo mpaka kumukwenya pakhosi. Apo anthu ena anafika pamalopo kuti amve chomwe mkuluyo amakwenyera mnyamatayo. Mwadzidzidzi mnyamatayo anazambatuka ndikuvumbwitsa zibakera zoonetsa nyenyezi ndi masana omwe mpaka njondayo kugwa pansi ngati chikuni chodyedwa ndi chiswe. Anthu ataleletsa ndeuyo mkuluyo wanenetsa kuti sadzayambiranso kuchita ndeu ndi achinyamata. Koma anthu adzudzula mnyamatayo akmba komenya munthu wachikulire ndipo ati atengera mnyamatayo ku bwalo la nyakwawa kuti akampayse mwambo wolemekeza akulu-akulu.

 

Malonda asokonekela ku Ndirande

Malonda anasokonekela dzulo pamalo ena ochitira malonda ku Ndirande kwa Chinseu mu mzinda wa Blantyre. Mtolankhani wathu yemwe anaona zonse zikuchitika wati mderalo muli atsikana awiri omwe amayendera limodzi. Ndipo mmodzi wa atsikanawo ali ndi malo ochitirta malonda pomwe amagulitsapo meshi komanso mafuta oziphodera. Ndipo miyezi itatu yapitayo mmodzi wa atsikanawo anakongola meshi ya 3 thousanda kwacha mu shop ya mzakeyo. Atatero mtsikanayo anaoswa mderalo. Koma dzulo laliwisili akuyenda mozemba amadutsa dera lina komwe mzakeyo anasamutsira malo ake ogulitsira malondawo. Mwini shopyo ataona mzakeyo akubwera potero adamulumphira ngati mphaka yemwe akugwira khoswe ndikuvula nzakeyo nsapato za gogoda zomwe anavala. Ndipo adamuudza kuti adzam’bwezera nsapatozo akapereka ndalama yonse ya meshi. Apo mwini nsapatozo anayeserela kuchondelera mzakeyo kuti amubwezere nsapatozo kamba sanazolowele kuyenda opanda nsapato. Anthu anali pamopo anangoti kakasi kusowa chochita. Mtsikanayo wanenesa kuti sazatenganso ngongole kwa anthu ena.

 


Mkamwini wina achita manyazi
Mkamwini wina akuyenda zoli-zoli ku Mtetete m’boma la Blantyre. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mderalo muli mkamwini wina yemwe ali ndi ngwa munchunu komanso salemekeza akuchikazi pakhomopo. Ndipo akayambana ndi mkazi wake nkhani za mnyumba iye amanamizira anthu ozugnulira pakhomopo kuti ndiwo omwe akusokoneza banja lake. Choncho masiku apitawo iye anapalana ubwenzi wa mseli ndi mkazi wina pafupi ndi pakhomopo. Ndipo chibwenzicho chitafumbira mkamwiniyo anagulira mkazi wachibwenziyo zinthu zosiyana-siyana mpaka kuiwala kusamala banja lake. Ndipo mkazi wake komanso achibale ake amkaziyo atadandaula, mkamwiniyo analalatira anthu onse pakhomo kuti ndi amphawi ndipo alibe chili chonse. Ndipo anapakira katundu wake ndi kubwerera kwao. Koma patangodutsa tsabata ziwiri mkamwiniyo anafikanso pakhomopo ati kuti apepese mkazi wake kuti abwerelane. Koma akuchikazi amanyetsa nkhwanga pamwala kuti mkaziyo asavomelenso mwamunayo kubwerela pakhomopo. Moti pakadali pano mkuluyo akuyenda ngati nkhuku yogwera mu vuwo.

Get Your Newsletter