11/07/17

Written by  Newsroom

Apasula banja yekha

Mkazi wina ku Bwanje m’boma la Ntcheu manja ali ku nkhongo atapasula banja lake ndi manja ake.

11
July

Chomwe chachitika nchoti mkaziyo anali pa banja ndi mwamuna wina ndipo zonse zimayenda bwino mpaka kukhala ndi ana awiri. Kenaka mwamunayo anapita ku John kukafuna maganyu ndipo anamutenga mkazi wakeyo kukamutula kwa makolo ake. Poyambilira zonse zimayenda bwino kamba koti mwamunayo amatumiza thandizo lokwanila ndipo mkaziyo amasangalala. Zimkuveka kuti mwamunayo wakhala zaka zitatu ali koyendako ndipo izi zinachititsa mkaziyo kuchoka ku khomo kwa mwamuna wakeyo ndikukukakhala kwa mai ake. Pamenepa mkaziyo anagonekera khosi kwa njonda ina yomwe imagaisa mchigayo china mderalo mpaka kugwa mchikondi. Anthu awiriwo akhala akuzemberana mpaka mkaziyo kukhala ndi mimba. Koma mphuno salota mwamuna yemwe anapita ku john uja anangotulukila mwadzidzidzi pa galimoto ndi katundu osiyana-siyana kuphatikiza chikwama cha mkaziyo momwe munali zovala zake. Koma mkazi-yo atamva kuti mwamunayo wabwera sansahitire mwina koma kuthawira ku phiri kuti akadzimangirile ndipo gulu lina la amai lomwe limalawila kunkhuni ndi lomwe linapulumutsa mkaziyi ali wefu-wefu chingwe chili m’manja.Pakadali pano mkaziyo ali m’manja mwa nyakwawa kuti afotokoze zifukwa zomwe amafuna kuzimangirila ngakhale iye akunenetsa kuti anachita izi kuti chuma cha ku John chisamudutse. Anthu ambiri akumuseka mkaziyo ponena kuti mapanga awiri avumbwitsa.

 

Mkulu wina abisala kudimba

Mkulu wina kwa Kachenga m’boma la Balaka akubisala ku dimba lina achitetezo akumufuna-funa kamba komuganizira kuti amafuna kumpha mzukulu wake m’masenga . Nkhaniyi ikuti mkuluyu amachita malonda ogulitsa mgrocery yina mderalo koma zithu sizimayenda bwino. Apa mkuluyu anaponda-ponda ku Mozambique ndipo sing’anga wina anawanamiza kuti akamphe mzukulu wake ngati chizimba cha mankhwalawo. Mkulu anachita zomwezo monga chizimba cha makhwalawo. Mwadzidzidzi nzukulu wawoyo anadwala mwakaya-kaya ndipo mai ake atapondaponda anauzidwa kuti amalume akewo akufuna kukhwimila mzukulu wakeyo kuti grocery yake iziyenda malonda ndipo kuti amafuna kugula galimoto. Izi sizinakomele mai akewo omwe anapita pa grocery pa mchimwene wakeyo ndikuyamba kumulalatila mpaka pakati pa usiku ndikumulonjeza kuti china chake chikangochitika mkuluyu awona chomwe chinameta nkhanga mpala. Pamenepa mkuluyu anangozemba mkuthawa mpaka pano sakuoneka ndipo grocery yakeyo ndiyoseka. Pakadali pano anthu ambiri asonkhana pa grocery ya mkuluyu ndipo akupempha komwe akubisala mkuluyu kuti afike kuti adzafotokoze chifukwa chomwe amafuna kumpha m’nzukulu wakeyo.

 

 

Mai wina alira ngati mwana ku Limbe
Mai wina ku Limbe mu mzinda wa Blantyre walira ngati mwana atsizina mtole ena atamukwanganula chikwama. Nkhaniyi ikuti lero laliwisili mai wina analowa mtauni ya Limbe kuti akagule zinthu zofunikira pokonzekera kubadwa kwa mwana yemwe m’bale wake akumuyebekezera. Paulendowo mai-yo anali ndi ka mnyamata koti kazimuthandiza kunyamula chikwama. Ndipo iye anayamba kutolela zinthu zofunikirazo monga, matewera, baby suit, mabotolo omwesera mwana mkaka zonse pafupi-fupi za 40 thousand kwacha. Atafika pa sitolo ina iye anasiila mwanayo chikwamcho ndikulowa mu sitoloyo. Koma panthawiyo nkuti mbava zina ziwili zikumuwerenga. Atalowa msitoloyo mbavazo zinafika pamalopo ndi kuba chikwamacho kenako osaonekanso pamalo. Mai-yo ataluka mu sitoloyo anapeza mwanyo diso lili psu! kamba kosowa pogwira chifukwa chakubedwa kwa chikwamacho. Apo onse awiri anayamba kulira ngati kwagwa maliro mpaka kuziponya pamatope. Pakadali pano mai-yo waopsyea kuti akhaulitsa amuna awili omwe akuwakaikila kuti amubela chikwama momwe munali matewela ndi baby suit za ndalama za nkhani nkhanizo.

 

Get Your Newsletter