10/07/17

Written by  Newsroom

Abindikila kamba ka manyazi
Mwamuna wina wochita bizinezi ya golosale ku Chikangawa m’boma la Mzimba akukhalira kubindikira nyumba chifukwa cha manyazi.

10
July

Mkazi wa mwamunayo wakhala akudzudzula paza khalidwe la nchuuno la mwamuna wakeyo koma iye amakanitsitsa paza mphekeserayo. Miyezi ingapo yapitayi njondayo inapalana ubwenzi wa mtseri ndi mtsikana wina wachichepere ndipo mkazi wa mwamunayo anazindikira za ubwenziwo. Koma pofuna kusungilana ulemu mkaziyo samamufunsa mwamunayo ponena kuti adzagwira yekha. Masiku apitawa mwamunayo anapangana ndi njoleyo kuti akakumane pa malo ena ndipo izi zinachitikadi koma osadziwa kuti anthu ena anawaona. Anthuwo pokwiya ndi zomwe njondayo yakhala ikuchita mderalo anakauza mkaze wake za nkhaniyi. Apa mkaziyo pamodzi ndi anthuwo anatsagana kuti akaone za malodzazo. Atafika pa tchirepo anapeza mkuluyo ndi mtsikanayo ali buno bwamuswe ndipo anthuwo kunali kumenya kosawamvera chisoni mpaka mwamunayo zinankoka manja mpaka kulephera kuthawa. Mwamunayo anachonderela anthuwo kuti awasiye koma m’malo mwake anangowalora kuti avale zovala zao ndikuwakokera ku bwalo la Nyakawawa. Ku bwaloko njondayo ndi mtsikanayo anavomereza za kulakwa kwao zomwe zinapangitsa kuti awakhululukire koma anawalipitsa chindapusa cha 10-thousand kwacha. Pakadali pano mwamunayo ndi mtsikanayo akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha nmanyazi, koma banja la njondayo laweyeseka.

Mayi wina adzudzulidwa
Anthu ena kwa gulupu Khoswe m’boma la Balaka adzudzula kwambiri mai wina pa zomwe wachita. Maiyo wakhala pa banja ndi mphongo ina yomwe imagaisa mchigayo mpakana kumangira nyumba ya malata maiyo. Miyezi ingapo yapitayi maiyo poona kuti zake zamuyendera anagwirizana ndi abale ake kuti athamangitse mkamwiniyo pa khomopo mu njira yomusemera chinyau. Nkhaniyi ikuti akuchikazi anayamba kupezera zifukwa mwamunayo mcholinga choti akawawidwa mtima achoke yekha pakhomopo zomwe mwanmunayo anazitulukira. Mwa zina akhala akumuloza chala kuti amachita zamatsenga komanso kusokoneza mabanja a weni zomwe anthu ambiri mderalo sakugwirizana nazo. Pa chifukwachi azilongo a maiyo amakhalira kulankhula zachipongwe mkamwiniyo akaledzera kabanga mpakana kumutukwana pa zifukwa zosadziwika bwino. Mkamwiniyo poopa kuti adzangofera za eni anatsanzika pakhomopo koma akudandaula kwambiri kuti anavutika kuomba njerwa ndikumangira mkaziyo mnyumba yabwino kwambiri. Aku chimuna nawo ati sasiila pomwepa koma kukatula nkhaniyi ku bwalo kuti bwalolo ndilo linga gamule. Chimene akufuna akuchimuna nkuti ngati kuli kotheka bwalolo ligulitse nyumbayo kuti waoyo aone polilira pambuyo pogawana ndalama.

 

Atsikana oyendayenda anjatidwa
Apolisi mboma la Nkhotakota agwila atsikana oyendayenda asanu ndi atatu powaganizila kuti avulaza mkulu wina wa zaka 23 pomubaya ndi mpeni. Malinga ndi wachiwili kwa m’neneli wa apolisi ku Nkhotakota Paul Malimwe mwamunayo poyambilila amakambilana ndi mkazi wina kuti akacheze pochita zadama koma kenaka anamusiya atasemphana ndikuyambanso kucheza ndi mkazi wina. Zimenezi zinakwiitsa mkazi oyamba uja ndipo pa chifukwachi anamema anzake omwe mogwilizana anayamba kulasa mkuluyo ndi mipeni. Malinga ndi Malimwe, panopa mkuluyo amugoneka pa chipatala cha boma ku Nkhotakota. Malimwe wati atsikana onsewo akaonekela kubwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu ovulanza munthu. Mkulu yemwe amuvulazayo amachokela pamudzi wa Kamtanga mdela Senior Chief Malengachanzi mboma lomwelo la Nkhotakota.

 

Mtsogoleri wampingo achita zochitisa manyazi
Mtsogoleri wampingo wina kwa gulupu Chibuli mdera la mfumu Ndamela m’boma la Nsanje ndi nkhuku yomwe madzila ake omwe. yemwe watumiza nkhaniyi wati kumeneko kuli mkulu wa mpingo wina yemwe mwana wake wa mkazi anamuthamangitsa ku banja. Ndipo mwanayo anabwerera pakhomo pa makolo ake kumakhala monga khale. Koma ali pakhomopo bambo ake amtsikanayo anayamba kudyerera maso pa mwana wawoyo mpaka kumunyengerela nkumagonana naye. Masiku apitawo mkazi wabamboyo anapezerera bamboyo pamodzi ndi mwana wakeyo ali mchikondi kumalo ena ogona alendo. Apo atakatula nkhaniyo kwa mikoko yogona zadziwika kuti njondayo inaumiliza kugonana ndi mwanayo atyi pofuna kupeza zizimba za ubusa wa mpingowo.

Get Your Newsletter