07/07/17

Written by  Newsroom

Malonda asokonekela

Malonda anatsokonekera masanawu pa msika wa Namphungo mdera la Mfumu Juma m’boma la Maulanje. Yemwe watumiza nkhaniyi wati pamalopo pali banja lina lomwe mai wabanjalo ndi wolimbikira kuchita malonda pofuna kudzipezera zosowa pamoyo wake.

07
July

Koma pomwe iye amakhala wotamganika kupezera banjalo zosowa mwamuna wake amakhala akumwa mowa mmalo omwela mowawo. ndipo lero mai-yo ali kumsika kochita malonda mkuluyo anakokera kubafa mwana wake wobereka yekha yemwe ndi wazaka zoposa makumi awiri. koma mai-yo anafika mwadzizi m’bafamu ndikupeza bambo wopanda manyaziyo akulimbana ndi mwana wakeyo. Apo mai-yo anafuula kuti anthu adzamuonetse malozawo. Anthu atafika pamalopo anagwira mkuluyo ndikumuyendetsa pamsikapo kwinaku akumukuwa kamba koti ndi nkhuku yomwa madzila ake omwe.


Mwamuna wina alaula mudzi

Mwamuna wina wa zaka 39 yemwe amasoka nsapato pamsika wina kwa Malota mdera la Mulaje Bale m’boma la Mulanje walaula mudzi. Nkhaniyi ili motere kuti mkulu wina yemwe anali mdziko la South Africa watsekula malo omwela mowa omwe anthu ambiri akuthamangirako kamba ndi obeba mderalo. Ndipo Lamulungu lapitali adzakhali a mkuluyo adakapapira mowa wachilendo omwe mwini maloyo akugulitsa. Ndipo mai-yo atakhuta anthu ena akufuna kwabwino adamukokera kunyumba kwake. Koma pathawi yomwe iye anali atatapatika mwana wa mchemwali wake anali akukhetsera dovu adzakhali akewo. Anthu akufuna kwabwino atakawatsiya adzakhali akewo mkulu wopanda manyaziyo anathamangira kunyumbako ndikugawana chikondi ndi maiyo. Koma atakomedwa iye sanathe kuchoka mnyumbamo mpaka mmawa wa tsiku lotsatira. Ndipo mmawa wa tsikulo anthu omwe analawira kuti akaone momwe mai-yo anadzukira anagwira pakamwa pomwe anapeza anthu awiriwo ali mbulanda pa kama ya maiyo. Apo anthu anadziwa kuti yalakwa. Pakadali pano mkuluyo akumuseka kuti walaula mudzi ndipo mikoko yogona yati ikokera njondayo mkanyumba komata.

 

Mawanja awiri asokonekela

Tili mdera lomwelo la Mulanje Bale mawanja awiri aweyedzeka. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mderalo muli mai wina yemwe mpaka dzulo anali pa banja labwino kamba mwamuna wake ndi bwana ku kampani ina mu mzinda wa Blantyre. Mwa zina banjalo limakhala mosangala mpaka kumanga nyumba ya njerwa zotentha ya malata, komanso mpanda thi pomwepo. Koma kamba kosakhutisidwa mkaziyo yemwe ali ndi ana anai akunjira anapalananso ubwenzi wamseli ndi mwamuna wina yemwenso ngokwatira ndipo amagwira ntchito yokonza magetsi pa estate ina m’boma la Thyolo. Ndipo chibwenzicho chitafumbira awiriwo anatailira ndikumakomana mopanda mantha koma samadziwa kuti mwini mkaziyo wamva za chibwenzicho. Ndipo dzulo laliwisiri mwina mwamunayo anafika pakhomo ndi kachitsisira ndipo anakwera mu mtengo wamango womwe uli pafupi ndi nyumbayo kuti athe kuona zonse zomwe zimachitika kumpandako. Mosaklalitsa mwamuna wakubayo anafika pakhomopo ndi majumbo azinthu zosiyana-siayana. Atafika kumpandako awiriwo anayamba kugawana chikondi koma osadziwa kuti mwini nyumba akuona zomwe zimachtikazo. Apo mwini nyumbayo anatsika mu mtengowo ndikuthamangira kumpandako komwe anapeza awiriwo atakolekelana miyendo. Ndipo anayamba kufafantha mwamuna wakubayo mpaka kumuchotsa mano awiri. Nkhaniyi itafika kwa ankhoswe abanjalo iwo analamula mwamunayo kuchita zomwe zingamuthandize. Mwamunayo wagumula nyumbayo ndikutenga njerwa zonse kuphatikizapo malata anyumbayo. Komanso naye mkazi wa mwamuna wakubayo wati sakumufunanso mwamunayo. Pakadali pano mabanja awiriwo atha.

 


Mai wina ayaluka
Mai wina anthu akumulodza zala kwa gulupu Nsiyaludzu m’boma la Ntcheu. Nkhaniyi ikuti mderalo muli mai wina yemwe kwa zaka zambirir wakhala akupindula ndi zipangizo za ulimi za ulele zomwe boma komanso mabungwe akhala akugawa. Koma chifukwa cha zovuta zina chaka chino dzina lake silinatuluke pa mndanda wa anthu omwe apindule ndi ntchitoyi. Ndipo izi zakwiitsa mai moti wakhala akutsindika kuti mvula siigwa mderalo ngati iye salandira thumba la feteleza wauleyu. Pakadali pano anthu mderalo ali ndi nkhwa chifukwa patha mwezi mvula isanagwe. Koma mikoko ina yogona yati ikokera maiyo pambali kuti imufufuze bwaino za nkhaniyi.

 

Mwambo wa maliro ulekela panjila

Mpingo wina unaleka panjira mwambo wa maliro mdera la mfumu Kabudula m’boma la Lilongwe. Nkhaniyi ikuti mderalo munachitika maliro masiku apitawo omwe anali achikhirisitu. Mwambo wonse unayamba bwino ndipo akwayala anakutumula nyimbo ngati angelo. Koma nthawi yotulutsa chitanda itakwana, mai wina anayamba kubwebweta kuti omwalirayo wasiya akatundu ake m’mbuyo ndipo ngati amoyo samutumudzira katunduyo mmudzimo anthu atha psyithi! Izi zinapereka chithunzithunzi choti omwalirayo anali katakwe pa zitsamba. Motero ampingo anabweza moto pakaimbidwe kao ati popeza zomwe anayankhula mai wobwebwetayo zinali zachikunja. Apo mkulu wampingo yemwe anatsogolera mwambowo analamula kuti ulaluki ukachitika kumanda kokha basi. Koma ali kumandako anthu anali odabwa kuona anthu awiri omwa anavala mikanda komanso zithumwa zamitundu- mitundu ndipo ananyamula zinthu zachilendo kuphatikizapo nsupa yamikanda komanso chithumwa chopuma kwinaku akuomba mmanja mwaulemu. Iwo anaponya akatunduwo mzenje asanaikemo chitandacho ndipo amayankhula kuti, “katundu wanu tabwera naye ndipo mlekeni mwanayo musamuphe. chonde tagwira mwendo.” Anthu omwe anali kumandako anali odabwa kamba malemuyo anali wokonda kupemphera kwambiri akali moyo. Apo mkulu wampingo sanachitire mwina koma kuudza khwimbi la anamalira kuti mpingo wake suputiliza mwambo wamalirowo kamba pachitika zachikunja.

Get Your Newsletter