05/07/17

Written by  Newsroom

Dalaivala akunthidwa atagwidwa akuchita zadama
Dalaivala wina ku Blantyre amukuntha kodetsa nkhawa mdela la Kwacha atamupezelela akuchita zachisembwere ndi mai wina mgalimoto lake.

05
July

Nkhaniyi ikuti dalaivala wina anatengana ndi mkazi pamalo ena omwela mowa pogwilitsa ntchito galimoto yakuntchito. Ndipo m’malo mopeza malo ochezela anagoti pafupi mpomwe wafika ndipo anaimitsa galimoto yake pa Njamba. Kenaka anapita kumbuyo kwa galimoto yakeyo nkumacheza ndi mkazi uja ngati banja. Mosakhalitsa panafika amuna ena omwe akuti anagwila mkuluyo ndikuyamba kumuphika kwambili m’menemo mkazi uja anali atathawa kale ali mbulanda. Naye dalaivala atapeza mpata anathawa kusiya galimoto yaku ntchito ili yokha. Kenaka anthu ena anakankhila galimotoyo pa maofesi ena komwe aku ofesi kwao kwa dalaivalayo adzaitenga. Panopa, komwe kwapita dalaivalayo sikukudziwika.

 

Maphunziro asokonekela ku Zomba
Maphunzilo anasokonezeka pa sukulu ina kwa Mikola mdela la mfumu Chikowi mboma la Zomba bambo wina wochokela pamudzi wa William mdelalo atayambitsa ndeu. Nkhaniyi ikuti mkulu wina ali ndi mwana yemwe amaphunzila pa sukulu ina mdelalo koma nthawi zonse akati akamete amakanitsitsa ndipo amaopsyeza aphunzitsi kuti atha kuwalodza. Koma ngakhale amapitiliza kubwela pa sukuluyo aphunzitsi ambili zimawanyasa polingalila momwe tsitsilo linakulila mpaka limanunkha. Lelo m’mawa mphunzitsi wamkulu anagwilizana ndi anzake mpaka anabweza mwanayo kuti akabwere pokhapokha atameta tsitsilo. Mwanayo atapita kunyumba anakauza bambo ake ndipo mosakhalitsa anakwezana njinga ndi mwanayo kupita ku sukulu komwe-ko. Kumeneko anakapeza aphunzitsi ena ndi ahead ali ndi zokambilana m’malo modekha mkuluyo analowa momwemo ndikutulutsa aphunzitsi akulu aja panja. Kenaka wachiwili kwa mphunzitsi wamkulu analowelela ndipo mkuluyo anathawa ataona kuti ana asukulu akungana ndi miyala kuti angomumaliza. Anthu ambili ati nkutheka kuti mkuluyo chilipo chomwe adamuchitila mwana wakeyo. Panopa anthu akumuloza loza mkuluyo mdelalo zomwe zachititsa kuti aziyenda njila zodula chifukwa cha manyazi.Nyakwawa zinjatidwa
Nyakwawa zingapo za mboma la Dedza azitsekela mchitokosi poziganizila kuti zakhala zikubela anthu mwachinyengo. Watitumizila nkhaniyi wati masiku apitawa mabungwe osiyanasiyana akhala akumapereka thandizo losisiyanasiyana pothandiza boma kuti anthu azikhala mokondwa. Koma nyakwawa zina m’malo moganizila anthu ao zimakonda kulemba maina abale ao ndipo anthu ambili akhala akuvutika osalandila thandizo nyakwawazo zikuthyolela pa lilime ndalama komanso katundu. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi mabungwe ena amapereka ndalama ndipo m’malo mopereka kwa anthu oyenelela nyakwawazo zimagawana ndalamazo. Koma kafukufuku atachitika malinga ndi madandaulo a anthu mdelalo zadziwika kuti nyakwawazo zaba ndalama za nkhani nkhani. Panopa, nyakwawa zoposa zinai azitsekela kale mchitokosi chifukwa choziganizila kuti zapalamula mlanduwo. Nayo mfumu ya ndodo komwe mafumuwo amachokela yaopsyeza kuti ithothola pa udindo nyakwawa zonse zomwe azipeze zolakwa pa mlanduwo. Pakadali pano zamveka kuti nyakwawa ina inalila kwambili pomwe amaitengela ku chitokosi ndipo inaulula kuti imalembadi abale ake okha okha. Momwe amawatenga nkuti anthu ena akuwakuwiza kuti anthu adyela.

 


Anyamata awiri asuzumilana ndi diso la nkhwezulu
Anyamata ena awiri okonza njinga zamoto pamsika wa kwa Nkando, mdera la Nkanda m’boma la Mulanje akuonana ndi diso lofiila. Nkhaniyi ikuti pa msikapo pali anyamata ena awiri okondana kwambiri ndipo onse anali ndi malo amodzi okonzela njingazo. Izi zakhala zikulimbikitsa ubale wa anayamatawo mpaka kumayenderana m’makomo mwao. Mwa zina akakhala ndi vuto awiliwo amamasukira ndipo amathandizana kwambili. Ndipo akazi anyamatawo amakhala bwino ngati pachibalenso. Pa chifukwachi anthu ambiri mderalo ankawayamika anyamatawo chifukwa chakhalidwe lao labwino. Ndipo kamba kolimbika pa ntchito anyamatawo akhala akupeza phindu lokwanira mpaka anaganiza zokuza bizinesiyo potsekula malo ena kwa Goliati m’boma la Thyolo. Pamenepa, m’modzi mwa anayamatawo anapita kwa Goliatiko kuti akayambe garaja yatsopanoyo ndipo anasiya mkazi wake kwa Nkando ndipo anapempha mzakeyo uja kuti apitilize kumayang’anira mkaziyo monga akhala akuchitira m’mbuyomu. Koma zomwe zadabwitsa anthu kumeneko ndi zoti m’nyamatayo atangochoka mderalo, mzakeyo wapalana chibwenzi ndi mkazi wake. Pakadali pano mwini mkaziyo wati wathetsa ubale wake ndi mzakeyo popeza ndi munthu waosadalilika. Ndipo anthu kumeneko akukaika kuti mwina ubwenziwo unayamba kale kale pomwe anthu ena akuseka mkaziyo chifukwa chodanitsa amuna awiliwo.

Get Your Newsletter