04/07/17

Written by  Newsroom

Akhadzuka chala cha wachitetezo

Mnyamata wina analuma ndikukhazuliratu chala cha wachitetezo wina ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre masiku apitawo.

04
July

Nkhaniyi ikuti mderalo muli mnyamata wina yemwe amachita geni pa malo okwelera basi a weaving. Ndipo tsiku lina ali pamalo panafika mnzake ndipo anagula zinthu za 100 kwacha ndikupereka 1000 kwacha. Atamupatsa change woguluayo anachoka pamalopo. Koma madzulo a tsikulo wogulitsa anakapapila mowa wachilendo ndikuyamba kuvutitsa mnzakeyo kuti sanamulipire pomwe anagula katundu pamale ake masanawo. Apo wiriwo anayamba kukangana. Koma atalephera kumvana bwino anyamatawo anayamba kutuwitsana ndi zibakera. Anthu omwe anali pamalopo analephera kuwaleletsa anyamatawo kamba amati iwo anachekera mangolomera. Koma ndewuyo itachema pamalopo panafika chiphona china chomwe chinafuna kuleletsa anyamatawo. Ndipo chinagwira mmiodzi mwa anayamatawo kuti chimukankhire kumbali. Mosakhalitsa chiphonacho chinayamba kulira ngati mwana chifukwa mnyamatawo adaluma ndikukhazuliratu chala. Pakadali pano, chiphonacho chanenetsa kuti chidzathana ndi mnyamatawo chikadzachira.

 

Anthu akhala mwa mantha kamba ka zamatsenga

Anthu ena akukhala mwa mantha kwa gulupu Goma mdera la mfumu yaikulu Dzoole m’boma la Dowa. Yemwe watumiza nkhaniyi wati kumeneko kwakhala kukuchita zinthu zamatsenga zochuluka.Mwa zina anthu akhala akumva anthu osaoneka akawaitana pakati pa usiku. Malinga ndi amene watumiza nkhaniyi ena akumaona m’nyumba zao mukuwala ngati muli magetsi chonsecho amakhala mnyumba zao zopanda magetsi. Anthu ena akhalanso akudandaula kuti m’mawa kukacha amapeza kukhomo kuli pululu chonsecho anatseka usiku wapitawo. Ndipo masiku apitawo kumeneko anthu anadabwa ndi chinthu china chachilendo chomwe chinagwa pamudzipo. Chinthucho akuti chinali ndi mapiko ngati mbalame, mutu wamaonekedwe odabwitsa koma chili ndi miyendo inayi ngati chifuyo. Mwini nyumba pomwe papezeka chinthucho wati aponda-ponda kuti anthane ndi anthu omwe akumuseweretsa m’matsenga. Anthu ambiri kumeneko ali ndi chikhulupiro kuti zinthuzo ndi zamatsenga.

 

Mkulu wina wanchiuno abeledwa njinga

Mkulu wina wa mchiuno kwa Chingagwe mboma la Balaka akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi chifukwa cha manyazi atamubela njika yake yakapalasa. Nkhaniyi ikuti mkuluyo kwanthawi yaitali wakhala akuzembera mkazi wake kwa nthawi yaitali. Koma anthu ena akuti akhala akumamulonda kuti aone momwe angamuphwetsele matama ake. Tsono masiku apitawa anauza mkazake kuti akupita ku msika koma chonsecho akupita ku chibwenzi. Mkulu uja akuti anafika pa shop ina pomwe anagula mpunga, mazila ndi mafuta kenaka anauyala ulendo ku chibwenzi chake. Koma amuna ena akuti anayamba kumutsatila pambuyo mpaka kukafika pomwe amayedzeka njinga yake. Mkuluyo atakalowa m’nyumba mwa mkazi uja amuna aja anangotenga njinga ija nkusowa nayo mdelalo. Mkulu uja atamaliza kucheza ndi mkazi uja anadzidzidzimuka kupeza kuti njinga yake yasowa. Pamenepa, anayamba kulila ngati waonekeledwa zovuta. Kufika kunyumba akusowa chouza mkazi ndipo m’malo mwake wamuuza kuti wabwereketsa kwa mkulu wina wa kabaza chonsecho lili bodza. Pakadali panopa, mkulu akubindikila m’nyumba chifukwa cha manyazi atadziwa kuti anthu akumulozaloza kuti wabetsa njinga kuchibwenzi. Mboma lomwelo la Balaka pamudzi wa Kanyoza mwamuna wina amukuntha kodetsa nkhawa atamutulukila kuti wakhala akubisalila amai akamasamba nkumawaonelela. Nkhaniyi ikuti amai ambili omwe amakonda kuchapa ndikusamba mu mtsinje wa Livilivi akhala akudandaula za bamboyo. Pa chifukwachi tsiku lina anagwilizana kuti amubisalile ndikumugwila. Pamenepa, zinathekadi ndipo amai ena amanamzila kuvula zovala zao pamene mkuluyo amafika. Amai ena anamuzungulila mpaka kumugwila ngati napiye apa akuti anayamba kumukuntha mpaka anamuvula zovala kupita naye kwa nyakwawa komwe zamveka kuti amulipitsa chindapusa.

 

Adzukulu asokoneza mwambo wa maliro

Mikoko yogona kwa Msilemba mboma la Kasungu yadzudzula zomwe achita adzukulu okumba manda posokoneza mwambo wa malilo chifukwa chadyela. Nkhaniyi ikuti adzukulu amadandaula kuti sadawapatse madzi osamba m’manja atamaliza mwambo oika malilo komanso kuti ati anawapatsa chakudya chochepa. Nkhani-yi inayambika adzukulu atayamba kudandaula kuti chakudya chomwe anamfedwa anapereka chinali chochepa ndipo zimenezi zinadzetsa mpungwepungwe mpaka kufuna kunyanyala kukumba mandawo. Koma akulu akulu ena anawalangiza kuti adzukulu omwe ali ndi njala akadye m’makwawo malinga nkuti chakudya chomwe anapereka chinali chokwanila koma kuti adzukulu ena amangopita kumanda-ko nthawi ya chakudya basi zomwe zimachititsa kuti omwe agwila ntchito asakhute. Koma adzukuluwo akuti aopsyeza kuti sadzagwila ntchito m’mudzimo ngati zina zitawagwela pokhapokha amfumu awapatse mbuzi imodzi. Koma anthu ambili ati zomwe akunena adzukuluzo nzopanda mutu ponena kuti nyakwawa ili ndi mphamvu yosankha gulu lina la adzukulu okumba manda aulemu.

Get Your Newsletter