30/06/17

Written by  Newsroom

Apasidwa makofi kamba kodyesa anthu nyama ya fisi
Mnyamata wina kwa Nkalo mboma la Chiradzulu amutuwisa ndi zibakera chifukwa chowadyesa anthu am’deralo nyama ya fisi powanamiza kuti ndi ya Ng’ombe.

30
June

Nkhaniyi ikuti tsiku lina mnyamatayu anafika m’derali ndi kanyenya wa nyama yomwe anaikonza komanso kuyikazinga mokhesa dovu. Chifukwa chamaonekedwe okhesa dovu a kanyenyayu, anthu amalimbirana ndipo ena amachita kumwera msuzi. Choncho Kanyenyayu sanachedwe kutha. Posakhalisa, mbiri inamveka kuti kanyenyayu anali wa nyama ya Fisi ndipo amanenawo ndi anthu omwe anamuona akumukonza fisiyo yemwe anaombedwa ndi galimoto mumsewu. Apa anthuwo sanayimve koma kumusakasaka mnyamata wachipongweyo ndipo anakamupeza akumwa delunde ndi ndalama zomwe anazipangazo. Atamufunsa za kanyenyayo, iye anati ndi wang’ombe yomwe anakagula pa msika wina kumeneko. Koma anthuwo anamuuza kuti patsikulo, pa malopo sipanaphedwe ng,ombe. Apa ndipomwe nyamatayo anawona kuti yalakwa koma kuwulula kuti kanyenyayo anali wa nyama ya fisi. Kenako anthu omwe anadya kanyenyayo anayamba kumuthizimula uku ena akupisa chala kukhosi kuti ati asanze. Tambwaliyo anayesesa kupepesa kwa anthuwo kuti amukhululukire koma iwo anapitilizabe kumukuntha mpaka kumusiya ali thyapsa. Anthu a mderalo, anenesa kuti sazagulanso kanyenya kwa mnyamatayo.

 

Nyakwawa ina igulisa malo amwini

Nyakwawa ina kwa Chitukula mboma la Lilongwe anayikokera ku bwalo lamfumu atayitulukira kuti inagulisa malo amwini kwa njonda ina yabizinesi. Yemwe watitumizira nkhaniyi wati Nyakwawayi yomwe ndiyokonda Kabanga, inapsa moti imasowa ndalama yomwera mowa. Ndipo tsiku lina ikucheza pabawo, nyakwawayo inamva kuti njonda ina yabizinesi mdera loyandikana nalo ikufuna malo oti igule. Iyo sinachedwe koma kuthamanga kukakomana ndi njondayo ndipo inamufotokozera kuti ili ndi malo ogulisa. Kenako awiriwa anatengana kukawona malowo. Atamvana mtengo, njondayo idaperekako theka la ndalama zomwe adagwirizanazo. Chifukwa choti nyakwawayo inakhalisa osalawako, inathamangira kokawutikita mowa mpaka kugona komweko masiku anayi. Kenako ndalamazo zitatha, nyakwawayo inabwelera kwawo. Koma chodabwisa ndi choti nyakwawayo imaoneka yosakhazikika ndipo ikamayenda, imakhala ili chewuchewu. Ndipo tsiku lina njonda yabizinesiyo inatenga anyamata oti akayambe kuumba zidina pamalopo. Ali mkati mokambirana, kunatulukira amuna ena awiri omwe anawafunsa chomwe amachita pamalopo. Njondayi itafotokoza kuti malowo ndi ake ndipo inachita kugula kwanyakwawa ya mderalo, amuna awiriwo anauza njondayo kuti malowo ndi a mmodzi mwa awiriwo. Kenako onsewa anatengana kupita kwa nyakwawayo. Nyakwawayo itawawona anthuwo, inangoyamba kuyankhula yokha kuti ibweza ndalamazo. Ndipo anthuwo atafunsa kuti ndalama zake ziti, nyakwawayo inafotokoza kuti malowo sanali ake koma inangopsa ndipo imafuna kulawako kabanga. Apa, anthuwo anayiduduluza nyakwawayo kupita nayo kwa mfumu yayikulu ya m’deralo komwe anakayidzudzula chifukwa cha khalidwe lonyansali. Omwe atitumizira nkhaniyi ati nyakwawayi yalonjeza kuti ibweza ndalamazo m’masiku khumi. Tikunena pano ati nyakwawayo ayimisa kaye paudindo wake ndipo ati ikuthamangathamanga kusakasaka ndalamazo kuti ibweze isanafike nthawi yomwe agwirizanayo.

 

 

Athotholedwa mumpingo kamba kokuba ndalama

Akuluakulu a komiti yoona za chitukuko pa mpingo wina kwa Kaduya mboma la Phalombe awathothola mu mpingo ataba ndalama za mpingo. Nkhani-yi ikuti akulukaulu ena apa mpingo-wo anazindikila kuti ndalama zina pafupifupi 30 thousand Kwacha komanso matumba a simenti awiri olemela anasowa. Choncho akulu a mpingo-wo pamodzi ndi abusa anatengela atsogoleriwo poduka mphepo ndi kuwafunsa mwaulemu za komwe ndalama ndi simentiyo zapita. Abusa akuti anuza akamunawo kuti abwenze zinthu-zo zinthu zisanafike poipa. Koma njondazo zinakana kubwenza zinthu-zo. Apa mbusa-yo sanachedwe koma kuchotsa anthuwo mu komiti ndipo patapita sabata zingapo angowachotselatu mu mpingo.

 

 

Atsikana ena akunthana ku Chilomoni

Atsikana ena awiri oyendayenda ku Chilomoni mu mzinda wa Blantyre akuthana mpaka kung’ambilana zovala atakomana pa malo ena pomwe anazindikila kuti akuyenda ndi mwamuna mmodzi. Mwamuna-yo akuti amagwira ntchito ya udalaivala ku kampani ina mu mzinda wa Blantyre. Tsono masiku apitawa njondayo ili pa malo ena ikupapila bibida idakukama ndi mtsikana wina woyendayenda ndipo mgwirizano wao udankelankela mpaka adamuchitila lendi nyumba ncholinga choti adzikhala yekha. Mkuluyo yemwe ali kale ndi mkazi ku nyumba adadyeleranso maso pa mtsikana wina woyendayenda ndipo tsiku lina onsewo adakumana pa malo ena achisangalalo. Ndiyetu atsikanawo anayamba kuchitilana nsanje mpaka kukwenyana. Chifukwa chakuledzela atsikana awiriwo anayamba kumenyana mpaka kung’ambilana zovala.

Get Your Newsletter