24/06/17

Written by  Newsroom

Asekedwa kamba ka nkhuli
Mwamuna wina akumuseka kwa Sub-T.A. Ngwelero m’boma la Zomba kamba ka nkhuli yomwe ali nao.

24
June

Nkhaniyi ikuti malinga ndi fisi olusa omwe awanda kumeneko, tsiku lina afisiwa anagwira galu m’mudzi wina. Ndipo munthu wina amene ali ndi khola pafupi ndikumene afisiwa alusa kwambiri anatuluka pofuna kupitikisa afisiwo. Atayesetsa kuwapitikisa afisiwo, anabwelera kukagona. M’mawa wa tsiku lomwelo, anayamba kutsatira mapazi afisiwo. Potsatira mapazi, anapeza chiwindi cha galu ndipo anachitola pomaganizira kuti ndi chambuzi. Mkazi wake anaphika mphafayo nkudyera nkhomaliro mosangalala. Koma madzulo ake a tsiku lomwelo anamva munthu wina dera lomwelo akudandaula kuti galu wake wagwidwa ndi afisi usiku wapitawo. Atapita kukatsimikiza anakhumudwa atawona mutu wa galu yemwe anajiwa ndi afisiwo ndipo mkazi wake anataya ndiwo zonse zomwe zinatsala mumpoto. Padali pano mkuluyo akuyenda wela-wela kamba anthu mderalo akungomutseka chifukwa cha nkhuli yake.

 

Asololedwa kunsi kwa bedi

Mnyamata wina amusolola pansi pa bedi yomwe anabisala kwa gulupu Kachenje mdera la mfumu yaikulu Kawamba m’boma la Kasungu. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mderalo muli mnyamata wina yemwe walemba mayeso a folomu fou chaka chathachi. Ndipo wakhala ali chitsanzo chabwino kwa anthu mderalo kamba nkoyamba kuti mnyamata wamsinkhu wake amalize maphunziro ake asekondale. Koma ngakhale ali wachichepre zadziwika kuti mnyamatayu saopa akazi ngakhale oti ali pa banja. Izi zatsindikizika masiku apitawo pomwe amupezerela pansi pa bedi yamkazi wa mwini. Pa tsikulo mwini mkaziyo adasanzika mkazi wake kuti apita ulendo wokagonera komwe. Apo mkaziyo anapeza mpata kuitana mnyamatayo. Mwadzidzi pakati pa usiku mwini mkaziyo anafika pakhomo kamba ulendo wake anusintha. Ndipo mwamunayo atgogoda pachitseko mkazi wake anachedwa kutsekula chitsekocho. Ndipo atathyola chitsekochoa anadabwa kuona mapazi akuonekera kunsi kwa bedi. Apo anamusolola pansi yabediyo ndikuyamba kumuphika mpaka nkhope yake kutupa ngati chitumbuwa cha nthochi. Pakadali pano mnyamatayo wasamuka mderalo kamba ka manyazi.

 

Mwambo wa maliro usokonekela
Mwambo wa maliro unasokonekela kwa agulupu Kasanje mdera la Makanjira m’boma la Salima. Nkhaniyi ikuti kumeneko nyakwawa ina inamwalira masikuta apitawo. Koma eni mbumba komanso mamulumuzana analephera kugwirizana za manda omwe akaikeko malemuwo. Ngakhale malirowo anayenera kuika patadutsa tsiku limodzi, malirowo atha masiku atatu asanawiake. Anthu ena ataona kuti njobvu zakolekelana minyanga pankhaniyi ena anakakoka mfumu ya ndodo ya mderalo kuti ilowererepo. Ndipo itafika pa siwapo mfumuyo inapempha achibalewo kuti amvetsetsane pankhaniyo ndipo kuti mbali ina iyenera igonje. Izi zinathekadi. Pakadali pano anthu mderalo adzudzula eni mbumbayo kamba kochedwetsa mwambo wa maliliro, koma ayamika mfumu ya ndondoyo kamba kozichepetsa kulangiza achibalewo.

 

Nyakwawa ichita chisembwele ndi mtsikana ozelezeka

Nyakwawa ina m’boma la Mchinji akuiseka kamba kochita chiwerewere ndi mtsikana wozelezeka ati pofuna zizimba. Yemwe watumiza nkhanniyi wati mderalo muli mtsikana wina yemwe amadwala matenda akugwa. Ndipo tsiku lina anachoka pakhomo pa makolo ake nanka nayenda uku ndi uko. Koma makolo ndi achibale a mstikakanayo anali odabwa kuona kuti mdima unayamba kugwa mtsikanayo asanafika pakhomopo monga achitira nthawi zonse. Apo achibalewo anaymba kusakasaka mtsikanayo koma anthu anali ndi chisoni pomwe anakomana ndi mtsikanayo akutuluka mnyumba ya nyakwawayo koma atanyamula andiloko wake mmanja. Ndipo mikoko yogona itachita kafukufuku zatsimikizika kuti nyakwawa yopanda manyaziyo inachitadi za chisembwere ndi mtsikana wodwalo. Ndipo mamulumudza ena ataipanikiza nyakwawayo yaulula kuti inachitadi zachipongwezo pofuna kukhwimila mpando wa unyakwawa. Pakadali pano anthu ena ati atengera nkhaniyi patali.

Get Your Newsletter