18/05/17

Written by  Newsroom

Chidakwa china chikupidwa makofi

Chidakwa china pa Neno Turn off m’boma la Neno chaona polekera atachithambitsa ndi makofi owonetsa nyenyezi.

18
May

Nkhaniyi ikuti miyezi ingapo yapitayo mwamunayo anaombedwapo ndi galimoto koma pa nthawiyo anali asanayambe kumwa kabanga. Atalandila ndalama zake zachipepeso mwamunayo anayamba khalidwe lakumwa mowa chifukwa choti samashota. Mwa zina mkuluyo anayamba kusowa pakhomo pake mpakana osafuna kusamala banja lake ndipo amakhala akuyendayenda ndi galimoto lake lomwe ena analipatsa dzina kuti phakasala. Tsiku lina atamwa mowa wa kabanga mwamunayo anayamba kulalatila aliyense mderalo kuti iye ndi mponda matiki uku akuyenda dzandidzandi mu msewu. Nthawi zina mkuluyo amagona mu mseu ndipo tsiku lina anagona mu msewu kuti lamba ndipo anthu ena anakanong’oneza akulu akulu aza chitetezo paza khalidwe la mwamunayo. Apa anthu oyang’anila za chitetezowo mderalo m’mawa lake anakapeza mkuluyo kunyumba kwake ndikuyamba kumumenya kolapitsa ndipo kumapeto kwake anamulipitsa 5-thousand kwacha. Anthu ambiri akwiya kwambiri ndi mkuluyo chifukwa chaza khaklidwe lake la nchuuno ndikusokoneza mabanja aeni chifukwa cha ndalama zomwe analandila zomupepesa chifukwa cha ngozi yapa msewuyo. Mwamunayo pakadali pano akuyenda mozemba chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi ndipo mkazi wake wayamba wachoka pa banjapo. Mwamunayo ati pakadali pano akukhalira kuchita maganyu okumba zimbudzi.

 

Ayenda zamadulira

Anthu ena kwa Kasumbu mboma la Dedza akuyenda njira zodula chifukwa cha manyazi kamba kazomwe achita. Masiku apitawa anthu a mderalo anali odabwa atapeza kuti gule wamkulu atamuunjika mu mseu. Nkhaniyi ikuti anthuwo pamodzi ndi guleyo ngakudabwe koma chifukwa chosagwirizana pa zinthu zina analondolerela gule wamkuluyo ku malo ena mpakana kukamuunjika pa mseu choncho chifukwa chopanda silambe omwe ndi maso agule anangokhala chete pa msewu. Mikoko yogona komanso anthu ena omwe amakhudzidwa ndi nkhani zakudabwe ati achita chilichonse mpaka afunefune anthuwo. Mphekesera itawapeza anthuwo zamveka kuti akubisala podziwa kuti akawatengela kudambwe akawaphika kwambili ndi zikwapu za moto zopaka tsabola.

Mnyamata otchuka akunthidwa

Mnyamata wina wotchuka pa sitolo zapa Mkando ku Mulanje analira ngati mwana anthu atamukuntha mpakana thapsya. M’nyamatayo yemwe amagulitsa mafuta masiku apitawa anashota ndipo m’malo mwake anapita kwa Chonde ndikukabera munthu wina njinga yakapalasa. Eni njingayo atafufuza za njingayo sanaipeze koma anthu ena anawatsina khutu kuti anamuona mnyamatayo ali ndi njingayo kwa Chonde uku akuitsatsa malonda. Apa anthuwo anamemana ndikukagwira tsinzinamtoleyo mpakana kuyamba kumuphaphalitsa ndi makofi zomwe zinapangitsa kuti m’nyamatayo ayambe kulira ngati mwana. Koma pa nthawiyo m’nyamatayo anaseketsa wanthu ponena kuti anachita izi pofuna kukweza bizinesi yake yogulitsa mafuta yomwe pakadali pano yatitimila. Pa chifukwachi anthu ena achifundo anapempha anthu omwe amamakuntha aja kuti amukhululukire pamene ena anatsindika kunena kuti ngati akufuna kuti amukhululukire ayambe walowa ku chitokosi.

 

Chipwilikiti pa bwalo la nyakwawa

Chipwilikiti chinabuka ku bwalo la nyakwawa ina mdera la Kamwendo ku Mulanje anthu omwe anali pa malopo atagwira m’modzi mwa othandiza a Nyakwawa pozenga milandu ndikuthambitsa ndi makofi. Nkhaniyi ikuti anthu ambiri m’mudzimo akhala akudandaula paza khalidwe la mkuluyo yomachita maubwenzi a nseli ndi akazi a weni chonsecho iye ngwapa banja. Anthu ambiri akhala akulangiza mkuluyo koma kwa nthawi yayitali samalabadila zolankhula anthuwo. Tsono pa tsikuli kunali mlandu ku bwalo la Nyakwawalo ndipo iye anali nawo pa gulu lothandiza kuzenga mlandu. Atayamba kulankhula anthu anamudzuma mkuluyo komanso kumukuwiza zomwe zinapangitsa kuti pa malopo pakhale chipwilikiti. Pofuna kuteteza mwamunayo nyakwawa ya mudzimo inapempha anthuwo kuti asunge bata koma m’malo momvera za pemphoro munthu wina anakatenga musi ndikuponyera wapa mpandoyo koma apa iye anadzambatuka mpaka kugwa ngati thumba la makaka. Apa mkuluyo ataona izi analiyatsa liwiro la mtondo wadooka uku akukuwa kuti ndikufa-ndikufa ndipo mlanduwo unasokonezeka chifukwa choti anthu ambiri anafa ndi phwete. Pakadali pano mwamunayo wachoka pa chikamwini pomwe amakhala nkubwerela kwao ndipo anthu ambiri ati apitiliza kufunafuna mkuluyo kuti amukhaulitse. Malinga ndi yemwe watitumizila nkhaniyi ati mwamunayo wakhala akunamiza akazi ambiri kuti adzigona naye mcholinga choti adziwalemba maina pakhala zithandizo zosiyanasiyana zoti anthu ovutika alandile mderalo.

 


Get Your Newsletter