16/05/17

Written by  Newsroom

Apasidwa makofi kamba kofuna kudzimangilira
Mwamuna  wina mdera la Mitundu ku Lilongwe waona polekera atamuthambitsa ndi makofi chifukwa chofuna kudzimangilira.

16
May

Nkhaniyi ikuti mwamunayo ndi mlesi wotheratu ndipo  pa chifukwachi wakhala akudalira mkazi wake pa umoyo wao wa tsiku ndi tsiku. Mkaziyo chifukwa chotopa ndi khalidwe laulesi la mwamuna wakeyo anayamba njira zodula ndikuchita maubwenzi a nseri ndi amuna ena. Nkhaniyi itamupeza mwamunayo inamukwiyitsa kwambiri ndipo m’malo mwake tsiku lina anatsanzika abale kuti akupita ku ulenje koma chonsecho  akukadzimangilira pa tchire lina.   Anthu ena osaka ndi omwe anapeza mwamunayo akuthatha ndi moyo ndipo apa sanachedwe koma kumpulumutsa mkuluyo.  Atagwa pansi anayamba kumukupiza pamene ena akumpatsa chakudya kuti atsitsimuke ndipo zinathekadi.  Atatsitsimuka m’malo moti amufunse bwino lomwe, anthuwo chifukwa cha mkwiyo anayamba kumufafantha ndipo mkuluyo analira ngati kwagwa maliro.  Mwamunayo anayamba kuchonderela kuti amusiye uku akulankhula kuti wachilapa.  Mikoko yogona komanso anthu ambiri adzudzula kwambiri mwamunayo kuti m’malo modzimvera chisoni ndi khalidwe lake la ulesi chifukwa chani amachita zombwambwana kufuna kudzimangilira. Nyakwawa ya mderalo yachenjeza kuti mwamunayo akadzayambilanso ndi khalidwe lakelo adzamusamutsa m’mudzimo.

 


Akunthidwa mpaka thapsya kamba kokuba
Achinyamata atatu   Ntauniship ya Ndirande mu mzinda Blantyre awafafantha mpaka thapsya atawagwila kuti anaba mondokwa.  Mtolankhani wathu yemwe waona izi zikuchitika wati  anyamatawo anakaba chimanga ku mpembu pakati pa usiku ndipo anakwanitsa kusenza matumba olemera makilogramu 50  ndikutuluka m’mundamo. Kenaka ali m’njira cha ma 3-koloko  kum’bandakucha anangoti gululu ndi gulu la achitetezo lomwe linawaphaphalitsa  ndi mafunso kuti afotokoze komwe anatenga chimangacho.  Pamenepa  achinyamatawo anasowa choyankha mpaka m’modzi wa iwowo anazemba mkuthawa. Anthu ena  anayamba kuthizimula akubawo   mpaka onse kukomoka  ndipo achitetezo anatengera mbavazo ku chipatala china mu mzindawo.  M’modzi mwa anyamatawo wanenetsa kuti sadzabanso ngakhale pakadali pano zamveka kuti   m’modzi wa anyamatawo wamwalira ndipo mzakeyo ali mwakaya-kaya.  Pakadali pano, nyakwawa ya mderalo yachenjeza kuti aliyense opezeka akuba chimanga  m;minda adzalandira chilango choyenelera.


Ataila mwana mchimbudzi
Mikiko yogona kwa Namphungo mdela la Mfumu Juma mboma la Mulanje yaima mitu mai wina atataila mwana mchimbudzi.  Watitumizila nkhaniyi wati mai wina mwamuna wake adamwalila chaka chatha. Koma asadamusudzule mayiyo anapezeka kuti ali ndi pathupi pa njonda ina.  Koma mayiyo pamodzi ndi abale ake amabisa pathupipo mpaka anachila ati poopa kuti akuchimuna samupatsa gao lake la katundu.  Koma mwana wa mayiyo anaulula za nkhaniyi kuti mayiyo akubisa khanda kuchipinda. Usiku watsikulo mayiyo anakataya mwanayo mchimbudzi ndipo alendi ataona zimenezi  anafalitsa nkhaniyi. Panopa, ngakhale nkhaniyi inali m’manja mwa achitetezo zamveka kuti yazizila ndipo walendi yemwe anafalitsa nkhaniyi amuuza kuti asamuke lisadafike Lachisanu pakhomopo.  Ngakhale zili chomwe-chi akuchimuna ati afufuza nkhaniyi kuti aone chomwe chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga.  

Get Your Newsletter