12/05/17

Written by  Newsroom

Asonkheza ndalama za malipiro ake 
Mikoko yogona kwa Nankhumba m’boma la Mangochi yapukusa mitu ndi zomwe wachita mkulu wina posokhetsa ndalama za malipilo ake chikhalilecho amalandila ndalama zina ku mabungwe komwe akugwira ntchito.

12
May

Nkhaniyi ikuti mkuluyu adamulemba ganyu yodikira chimanga cha mabungwe ndipo amalipidwa ndalama zokwanila. Koma chokhumudwitsa nchakuti masana mkuluyu amayenda khomo ndi khomo kukadandaula kuti amumvere chisoni ndikumupatsa ufa kapena ndalama ngati malipilo ake kamba koti sakulipidwa. Anthu ena anakwiya ndi nkhaniyi mpaka anakakomana ndi eni mabungwewo omwe anawatsimikizila kuti mkuluyu akumulipila ndalama zambiri pafupifupi 25-thousand Kwacha. Pamenepa anthuwo anagwirizana zomukhaulitsa ndipo atafika kuti akatolere ndalama, nyakwawa ya m’mudzimo inalamula kuti amugwire ndikumumangilira pansi pa mtengo ndikukatenga eni mabungwewo. Kenaka m’modzi wa eni mabungwewo analamula mkuluyo kuti asabwerelenso ku ntchito kutanthauza kuti ntchito yake yauma. Pakadali pano mkuluyu akuyenda zoli-zoli chifukwa cha manyazi zitamveka m’mudzimo kuti amafuna kumabera anthu dzuwa likuswa mtengo.

 

Nyakwawa iwophyeza anyamata ena

Nyakwawa ina kwa Mtonga mboma la Salima yachenjeza kuti ikhaulitsa anyamata ena omwe anavala gule wamkulu ncholinga chofuna kubela anthu. Nkhani-yi ikuti m’mudzimo munachitika malilo amkulu wina ometa gule wamkulu. Pa chifukwachi mwa mwambo gule osiyanasiyana anatuluka m’mudzi kukasonkhetsa nkhuni ndi zina. Koma anthu anadabwa ndikuchuluka kwa gule wa Kamano yemwe amathyola miyendo ya nkhuku ndi abakha mkumakwapatila ulendo nazo ku dabwe. Zimenezi zinakwiitsa anthu ambili mpaka anafufuza nkhaniyi ndipo zinadziwika kuti panali gule wamkulu mutatu wa chinyengo. Nyakwawa itafufuza inapeza kuti ndi anyamata ena atatu akuba omwe anangovala nao gule wamkulu pofuna kubela anthu pa malilowo. Panopa, anyamatawo omwe maina ao adziwika athawa m’mudzi pooka kukawatsekela ku chitokosi cha apolisi.

 

Aba ndowa za ufa wa soya

Makolo ozungulila sukulu ina ku Lisasadzi mboma la Nkhotakota akwiya ndi zomwe mphunzitsi wina akuchita pakuba ndowa za ufa wa soya ndi matumba atatu omwe amaphikila ana. Nkhaniyi ikuti anthu akhala akudandaula kuti ana akhala akumadya phala lotepeta nthawi zonse ndipo ophika phala akafunsa mphunzitsi wamkulu amayankha m’maso muli gwaa! kuti ana akumadya kwambili ufa watha. Koma tsiku lina m’mawa anaona mphunzitsi wamkuluyo akutulutsa matumba aufa wa soya kupatsila anthu ena. Atamufunsa akuti anayamba kupanga chibwibwi zomwe zinapangitsa anthu kudziwa kuti mkuluyo ndiye wakhala akuba ufa wa phala la soya. Panopa, makolo mdelalo ati akufuna mkulu waza maphunzilo mdelalo aone chochita ndi mphunzitsi-yo asadatengele maganizo ao. Panopa, mphunzitsiyo wamkuluyo akuyenda ali wela wela chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi atadziwa kuti anthu akumulozaloza.

Get Your Newsletter