07/05/17

Written by  Newsroom

Mabanja asemphana kamba ka ufumu

Mabanja awiri achifumu kwa Santhe m’boma la Kasungu omwe ngapapachibale akukhalira kulalatilana tsiku liri lonse pa nkhani yaza ufumu.

07
May

Nkhaniyi ikuti mabanjawo kwa nthawi yayitali akhala akulimbilana pa yemwe angatenge ufumu. Koma nkhaniyi atayikambilana mbali imodzi ndi lomwe linavomerezedwa kuti litenge ufumu. Izi zinautsa mkwiyo waukulu ku mbali inayo ndipo posafuna kugonja akukhalira kutukwana amzawo tsiku ndi tsiku. Mfumu ya mderalo itamva izi yalangiza banjalo kuti ngati silisintha paza mtopolawo ayisamutsa mdera lake. Banjalo lamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sachoka chifukwa choti pa nkhaniyo sipanachitike chilungamo. Pamene timalandila nkhaniyi mkuti mbali inayo nalo lanenetsa kuti sagonjera za zomwe akuganiza anzawowo. Pakadali pano mfumu ya ndodo yaophyeza kuti aliyense yemwe samva malangizo amulipitsa chindapusa komanso kumukokera ku khothi.

 

Mai wa businezi adabwisa anthu
Mai wina yemwe amachita bizinezi yophika nsima pa msika wapa Kafele mdera la Kachere m’boma la Dedza akudabwitsa anthu pa zochita zake. Mwa zina maiyo wakhala akudziwika ndikupemphera kwambiri komanso nthawi yomweyo watchuka ndi nkhani zolanda amuna a weni. Maiyo ati akugwiritsa mau oti osamakanana ati ponena kuti bola munthuyo akutambasula manja. Pamene timalandila nkhaniyi nkuti maiyo ali pa ubwenzi ndi mwamuna wa msinkhu wa agogo ake. Akamufunsa iye amayankha m’maso muli gwa kuti nkhalamba ndi zomwe zimasunga wanthu. Maiyo wafika posambuka pomuuza mwana wake wa mkazi kuti asadzayerekeze kukwatiwa ndi anyamata omwe nthawi zonse amakhala khwakhwakhwa. Koma chodabwitsa mchakuti maiyo akayamba kupemphera malirime anthu amadziwa kuti pali munthu wa mai pa nkhani za Ambuye koma chonsecho akukhalira kulanda amuna a weni. Mikoko yogona komanso akuluakulu apa msikapo achenjeza maiyo kuti akapitiliza ndi khalidwe lakelo amusamutsa pa msikapo koma iye akumalankhula mwa thamo kuti sizitheka ati chifukwa choti nkhalambayo ndi m’modzi mwa akuluakulu akomiti yapa msikawo.

 

Mai wina asambitsidwa makofi
Mai wina mdera la Malemia m’boma la Nsanje analira ngati kwachitika maliro anthu ena atamuthambitsa ndi makofi chifukwa cha kuba. Nkhaniyi ikuti banja lina lomwe limakhala moyandikana ndi mayio lakhala likudandaulira mzaoyo kuti abakha awo akukhalira kusowa ndipo mai wakubayo naye wakhala akunena kuti akadzapeza yemwe akuchita izi adzathana naye chonsecho iye ndi amene amasowetsa zifuyozo ndikukhwasula. Paja pali mau oti padziko palibe chinsinsi. Tsiku lina mdzukulu wa mayiyo mosazindikira pamene amasewera ndi amzake anayamba kudzitamandila kuti iwo amakhalira kudya ndiwo za mkhwiru ponena kuti akhala akudya abakha onona okhaokha. M’modzi mwa anawo yemwe ngakubanja lija kwakhala kukubedwa abakha anakafotokozera bwino lomwe agogo akewo. Apa agogowo sanaimve koma kumema mikoko yogona kuti ikafufuze za nkhaniyi ndipo mwa mwai anakapezadi kuti mphika unali wodzadza ndi nyama ya bakha. Apa anthu omwe anasonkhana ku maloko kunali kumenya kolapitsa mpaka maiyo analira momvetsa chisoni. Koma anthu ena ofuna kwabwino anabweza ndalama zonse zolingana ndi abakhawo. Maiyo pakadali pano akukhalira kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi.

Get Your Newsletter