05/05/17

Written by  Newsroom

Nyakwawa iimitsidwa udindo kamba ka nchiuno

Nyakwawa ina kwa Kaduya ku Phalombe ayamba ayimitsa pa udindo chifukwa chowilikiza khalidwe lake la mchuuno.

05
May

Nyakwawayo akhala akuidzudzula chifukwa chokhala pa ubwenzi wa nseli ndi msuweni wake wapa banja koma iyo malangizowo imaponyera ku nkhongo. Masiku apitawa Nyakwawayo mopanda manyazi komanso mantha inapita kunyumba kwa msuweni wakeyo mwamuna wake ali konko . Atafika pa khomopo anapempha mwamunayo m’maso muli gwa kuti akufuna mkazi wakeyo akamuitanile chibwenzi chake zomwe mwamunayo anazindikira kuti linali bodza. Potopa ndi khalidwe la Nyakwawa-yo mwamunayo anagwira nyakwawayo ndikuyamba kuiminitsa ndi zibagera zoonetsa nyenyezi. Apa nyakwawayo inagwa pansi ngati thumba la nandolo uku ikuchonderela kuti ayisiye koma sizinamveke. Malinga ndi yemwe watitumizila nkhaniyi ati anthu omwe anasonkhana kudzaona malodzawo anawowoza nyakwawayo uku ena akupitiliza kuithidzimula kolapitsa. Anthu ena akufuna kwabwino anapempha gululo kuti ayikhululukire koma sizinamveke chifukwa ati kupatula nkhani ya nchiunoyo nyakwawayo yakhala ikusokoneza zambiri zokhudzana ndi umoyo wa anthu mudzimo. Pamene timalandfila nkhaniyi nyakwawayo ayamba ayimitsa komanso ikukhakhalira kubindikira nyumba chifukwa cha ululu komanso manyazi.

Wakaba afuna kuzembetsa munthu
Mnyamata wina wakabaza mdera la Mwaulambiya m’boma la Chitipa akunong’oneza bombono chifukwa chofuna kuzembetsa munthu. Myamatayo yemwe ndiwotchuka kwambiri pa ntchito yake anagwirizana ndi mtsikana wina wapa sukulu ya sekondale yoyendera kuti akamusiye kwao. M’malo mokamusiya kunyumba mnyamatayo anasintha njira kulunjika ku malo ena zomwe zinayamba kukaikitsa mtsikanayo. Mtsikanayo ataona kuti mtunda ukukula anayamba kukuwa zomwe zinapangitsa anthu kugwira mnyamatayo. Apa anthuwo sanachedwetse kuonetsa mkwiyo wao ndipo anayamba kuthambitsa wachiwembuyo ndi zikwapu uku ena akumugenda ndi miyala komanso zidutswa za njerwa. Gulu la anthu aza chitetezo mderalo linayesetsa kulanditsa mnyamatayo ndikumutengera ku polisi. Pakadali pano anthu ati akuda nkhawa ndi zomwe zachitikazo ndipo ayamba kukaikira kukwera njinga za kabaza za mderalo. Komabe akabaza a njinga za moto komanso akapalasa atsimikizila anthuwo kuti asakhale ndi mantha pa nkhaniyi chifukwa achita chili chonse kuthetsa khalidwe laupandulo mothandizana ndi achitetezo.

 

Dalaivala achita zodabwisa

Anthu omwe anakwera minibasi ina ya pakati pa Limbe ndi Blantyre kudzera ku Nkolokosa anaseka kosalekeza pa zomwe anachita dalaivala ndi kondakitala wake. Chomwe chinachitika minibasiyo itafika pa siteji ya Kwacha kuchokera ku Limbe kondakitalayo anapempha mzakeyo kuti ayambe wakataya madzi zomwe sizinasangalatse dalaivalayo. Pa chifukwachi dalaivalayo anazazila kondakitalayo kuti asatero chifukwa galimoto ina yomwe imabwera mbuyo mwao iwatengera anthu. Apa kondakitayu pofuna kumvela anakwera msangamsanga koma mwatsoka anthu omwe anali pa siteji yotsatila anatengedwa ndi minibasi ina ndipo dalaivalayo anadandaula momvetsa chisoni zomwe zinapangitsa kuti pasakhale kumvetsetsana pakati pao. Apa mofulumila kondakitayo analumpha ndikukodza mosasamala za anthu koma anali asanauze mzakeyo. Atayenda mtunda pang’ono anazindikira kuti kondakitalayo watsala zomwe zinapangitsa anthu omwe anakwera minibasiyo kufa ndi chikhakhali pamene ena anadzudzula dalaivalayo kuti anamulakwira mzake komabe anamudikira ndikumutenga. Pa chifukwachi anthu analangiza ndikudzudzula dalaivalayo kuti sizoona kuti angakanize mzakeyo kutaya madzi mcholinga choti apeze ndalama. Anthu pa ulendo onsewo amaseka zomwe analankhula dalaivalayo kuti lero akungokhalira kumenyedwa mimba kunena kuti sizikuwayendera. Komabe anthu ena ati akuganiza kuti kondakitalayo anali atamwa mkalabongo.

Get Your Newsletter