03/05/17

Written by  Newsroom

Ofulula mowa asatsa anthu
Omvera mau a Mulungu amalimbikitsa kuti tidzikhala opereka mcholinga choti tidzilandilanso zambiri, Koma nthawi zina mpofunika kusamala ndi zithandizo zina.

03
May

Izi zili chonchi malingana mkuti anthu ambiri akomana ndi vuto lalikulu mdera la Nankumba ku Mangochi atamwa mowa wa kabanga omwe anapatsidwa ndi munthu wina wofulula mowa mderalo. Pa tsikulo munthuyo anapereka zigubu zisanu mziwiri kwa makasitomala ake ati powathokoza kuti amamugula mowa ochuluka koma chonsecho mwamunayo ndi kanga ndi wamba sanaperepo mowa wa ulele kwa anthu chiyambireni ntchito yake yophika mowa pa zaka zambiri zapitazo. Makasitomalawo m’malo mofufuza bwino lomwe za mowao anangoti laponda la mphawi ndikuyamba kupapila mowao ndipo kumapeto kwake ambiri analedzebwa mpakana thaphya ndipo ena a iwo mpakana kukomoka. Pakadali pano anthu okwiya ndi nkhaniyi anakaononga bar la mwamunayo koma anthu ena mderalo adzudzula anthuwo pokachita za chipolowezo ati chifukwa choti mbiyang’ambezo zinakaputa dala dala satana ndi maukulu ake. Pamene timalandila nkhaniyi ena mwa anthuwo awatengera ku chipatala ndipo mwini balayo wathawa mderalo mphekesera itamupeza kuti akumufunafuna kuti amukokere ku bwalo la milandu.

Mwamuna wina alodzedwa dzala ku Machinjiri
Mwamuna wina ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre akumulozerana pazomwe wakhala akuchita mderalo. Mwamunayo wakhala ali pa ubwenzi wa ntseri ndi mkazi wa mwini ndipo mwini mkaziyo sanavute koma kulandula mkaziyo kuti akamange ukwati ndi mwamuna mzakeyo. Pa chifukwachi mkaziyo anakayambadi banja latsopanolo ndi njondayo koma chodabwitsa anthu awiriwo akhala akubweranso pakhomopo ndikudzavutitsa zomwe zakhala zikudabwitsa mwini khomoyo. Masiku apitawa ataona kuti mnyumba mwao mwalowa njala anapita pakhomopo ndikukathyola mondokwa zomwe zinakwiyitsa mwini nyumbayo kuti mpakana anangozula munda onse. Pa tsikulo ndeu ya fumbi inabuka koma anthu ambiri anadzudzula mwamuna wa nchuunoyo kuti ndiwombwambwana ponena kuti akanakhala mwamuna weniweni sakanachita zomwe akuchitila mwamuna mzakeyo. Mikoko yogona komanso anthu ambiri mderalo achenjeza banja latsopanolo kuti likapitiliza ndi khalidwe lao lopusalo aona chomwe chidameta nkhanga mpala.

 

Atha mnyumba mwao kamba ka mantha
Akulu-akulu a mpingo wina ku Luwerezi ku Mzimba athawa mnyumba zao chifukwa chochita mantha kuti anthu mderalo awathidzimula. Anthu amu mpingowo akhala akukaikira agulupa awo kuti akahala akumayenda ndi akazi a eni. Masiku apitawa atumiki a Mulunguwo anagwirizana ndi amai atatu amu mpingowo omwe ndi okwatiwa kuti akakumane nawo usiku. Anthuwo anauza zibwenzizo kuti akanamize amuna awo kuti akukatumikira alendo omwe anafika ku kachisiyo zomwe zinali za bodza. Amuna amaiwo atadabwa ndi kuchedwa kwa akazi awo anapita ku kachisiko ndipo anagwira pakamwa atapeza kuti akazi awowo ali pa chikondi ndi agulupawo nthawi ili cha m’ma 9-koloko usiku. Anthuwo sanachedwe koma kukuwa zomwe zinapangitsa anthu ambiri kusonkhana. Apa anthuwo anagwira akuluakulu a Mulunguwo ndipo kunali kumenya kwa mtima bii mpaka onse analira ngati ana. Mwa mwai akuluakulu a mpingowo anapeza mwai wothawa koma pakadali pano sakudziwika komwe apita. Malipoti ati anthuwo akuchita mantha kubwerela mnyumba zao kuopa mkwiyo wa anthu pa nkhaniyi. Mwa anthuwo ndi kwaya masitala, Deacon komanso komanso mkulu wina wampingo.

Mphongo zina zinenetsa kuti zaleka kuba
Mphongo zitatu mdera la Phambala ku Ntcheu zanenetsa kuti zaleka khalidwe lao lakuba anthu mderalo atazionetsa zakuda. Nkhaniyi ikuti amuna atatuwo anakalowa m’munda mwa munthu wina kukazula chinangwa pafupifupi ma ekala atatu usiku. Koma pa nthawiyo nkuti mwini munda-wo akuona zonse zomwe zimachitika ndipo chimene anachita nkuimbila anthu aza chitetezo koma mbalazo sizimadziwa. Posakhalitsa gulu la anthu linazungulira amunawo ndipo kunali kuwaphika moti m’modzi mwa mbavazo inalira ngati kwachitika maliro uku zili ndi mabala okhaokha a dzikwapu. Mwini mundawo sanalekere pomwepo koma kuuza anthuwo kuti apake mbavazo chimbudzi cha nkhumba thupi lonse ndipo zinachitikadi. Pamene amakokera ku bwalo amunawo nkuti ali ndi fungo losaneneka la ndowe la nkhumba. Ku bwaloko anawalamula anthuwo kuti alipire 5-thousanda kwacha aliyense komanso akhale akulima m’mundamo kwa sabata la thunthu ndipo Nyakwawa inachenjeza kuti ngati sachita zimenezo awapititsa ku polisi. Anthuwo pochita mantha ndiku chitolokosi anavomereza za chigamulocho. Pakadali pano amunawo akuyenda monyowa ngati nkhuku yogwera mvuwo chifukwa choti nkhaniyi yawanda mdera lonselo.

Get Your Newsletter