02/05/17

Written by  Newsroom

Anthu atuluka mu mpingo
Anthu ambiri opemphera pa mpingo wina pa Neno Turn off mboma la Mwanza atuluka mu mpingowo chifukwa chaza khalidwe la mkazi wa mkulu wapa mpingowo.

02
May

Nkhaniyi ikuti mkazi wa Mkulu wa mpimgowo wakhala akulankhula nkhani zambiri za bodza zopekera mamembala amu mpingowo zomwe sizikhala zoona. Komiti yayikulu yapa mpingowo inaitanitsa ku bwalo mkazi wa mkulu wa mpingowo koma anakanitsitsa kukaonekera ku gululo ndipo m’malo mwake anayamba kuzazila anthuwo uku akuwalalatila. Mwa zina maiyo wakhala akunamizila amai amzao kuti ndi mahure komanso anthu akuba zamu mpingo chikhalireni maiyo ndi yemwe ali ndi mbiri zoipa zambiri monga kukhala pa ubwenzi wa ntseri ndi akuluakulu ena apa mpingowo. Pa chifukwachi mamembala ambiri akhala atuluka mu mpingowu pokwiya ndi zomwe maiyo wakhala akuchita. Anthuwo ati akutulukanso mpingowo chifukwa choti mkulu wa mpingowo wakhala asakuchitapo kanthu akamufotokozera za khalidwe la mkazi wakeyo. Maiyo ati akumalankhulanso mwa thamo kuti anthu akhoza kuchoka chifukwa sakuwasowa. Pakadali pano aku likulu la mpingowu achenjeza mkulu wa mpingoyo kuti malipoti omwe alandila ngati ali owona sachitila mwina koma kumuchotsa mtumiki wa Mulunguyo pa udindowu.

Mai oyendayenda adutsa njira zamadulira

Mai wina oyendayenda ku Mponela mboma la Dowa akuyenda njira zodula atazindikira kuti anthu akumufunafuna. Anthu a mderalo akhala akumudzudzu maiyo chifukwa chaza khalidwe lake lomenyanitsa mphongo. Kwa nthawi yayitali maiyo wakhala akulankhula mwa thamo kuti sivuto lake koma kuti amuna ambiri apa banja amatsatila kukongola kwake ndipo izi zakhala zisakusangalatsa anthu ambiri apa banja makamaka amai a mderalo. Masiku apitawa mai wachimaso-masoyo anagwirizana ndi njonda ina kuti akakumane ku malo ena ogona alendo ndipo zinachitikadi. Pamene izi zimachitika njonda inanso yomwe inali pa ubwenzi wa ntseri ndi maiyo imaona zonsezo ndipo m’malo mwake anakadikirila anthuwo pafupi ndi pa chipata cholowera ku maloko pamodzi ndi anyamata ena adzitho mcholinga chofuna kuthana ndi anthuwo. Patadutsa maola awiri anthu opanda manyaziwo anatulukira pa malopo ndipo mwadzidzidzi anangoti gululu ndi anthuwo ndipo apa ndeu ya fumbi inabuka ndipo anthuwo kunali kumenya kolapitsa mwamuna ndi maiyo. Mwa mwai maiyo anapeza mpata othawa zomwe zinapangitsa kuti njondayo zimutsalire ndipo anayimenya kwa chakwanu leka mpaka kuivulaza. Apa eni apa malopo atamva mfuu ndikulira kodabwitsa kwa njondayo anafika pa malopo ndikuyamba kuleletsa ndeuyo ndipo kumapeto kwake anatengera mwamuna wa nchuunoyo ku chipatala. Pamene timalandila nkhaniyi anthu omwe achita izi anathawa pa malopo ndipo eni malowo akupitiliza ntchito yofunafuna maiyo kuti amukokere ku bwalo la milandu chifukwa chodzetsa chisokonezo pa malopo komanso kuvulazitsa munthu. Koma anthu ambiri alangiza eni malo ogona anthu apa ulendo kuti adzionetsetsa kwathunthu ndikufufuza za anthu omwe amafika pa malo awo.

 

Mnyamata wina otchuka akunthidwa 
Mnyamata wina wotchuka pa sitolo zapa Mkando ku Mulanje analira ngati mwana anthu atamukuntha mpakana thapsya. M’nyamatayo yemwe amagulitsa mafuta masiku apitawa anashota ndipo m’malo mwake anapita kwa Chonde ndikukabera munthu wina njinga yakapalasa. Eni njingayo atafufuza za njingayo sanaipeze koma anthu ena anawatsina khutu kuti anamuona mnyamatayo ali ndi njingayo kwa Chonde uku akuitsatsa malonda. Apa anthuwo anamemana ndikukagwira tsinzinamtoleyo mpakana kuyamba kumuphaphalitsa ndi makofi zomwe zinapangitsa kuti m’nyamatayo ayambe kulira ngati mwana. Koma pa nthawiyo m’nyamatayo anaseketsa wanthu ponena kuti anachita izi pofuna kukweza bizinesi yake yogulitsa mafuta yomwe pakadali pano yatitimila. Pa chifukwachi anthu ena achifundo anapempha anthu omwe amamakuntha aja kuti amukhululukire pamene ena anatsindika kunena kuti ngati akufuna kuti amukhululukire ayambe walowa ku chitokosi.

Get Your Newsletter