27/04/17

Written by  Newsroom

Mai wina asowa mtendere kamba ka dama

Mai wina mdera la Nsamala ku Balaka akusowa mtendere chifukwa cha zomwe wachita. Maiyo yemwe mwamuna wake anapita ku Joni zaka zapitazo amakhala pa lendi mogundizana nyumba ndi banja lina.

27
April

Pa chifukwachi mwamuna wa mnyumba inayo anadyerela maso maiyo ndipo anapalana ubwenzi wa mtseri potengera mwai woti mwamuna mzake ali kunja. Paja pali mau timati lafote limakwana tsiku lina mai wachimasomasoyo analemba uthenga wapa foni kwa chibwenzi chake pomufunsa kuti KODI HONEY LERO UBWERA, koma mwa tsoka uthengawo unafikira mkazi wa njondayo uku mwamunayo ali ku bafa. Apa maiyo sanafune kuchita zachipolowe koma kufunsa mwa mtendere mzakeyo pokhala kuti nambala ya foni ya mzakeyo amaidziwa. Mai wa chimasomasoyo anasowa cholankhula ndipo anasowa mtendere uku akutuluka thukuta losamba ndipo mwadzidzidzi anachoka pa malopo osatsazika. Choseketsa pa nkhaniyi mchakuti maiyo amachoka m’mawa ndikubwera madzulo anthu atagona chifukwa cha manyazi. Izi wakhala akuchita kwa mwezi wathunthu. Pamene timalandila nkhaniyi anthu ena omwe anazindikira za nkhaniyi anadziwitsa mwamuna wake mdziko la South Africa-lo ndipo sizikudziwika kuti nkhaniyi itha bwanji.

Nyakwawa ina ichita manyazi
Nyakwawa yina mdera la Pemba ku Salima ikuyenda njira zodula chifukwa cha manyazi pa zomwe yachita. Kwa nthawi yayitali anthu mderalo akhala akuidzudzula nyakwawayo paza khalidwe lake yotumikira maubwenzi a ntseri. Masiku apitawo mbusa wina wotchuka pogawa mau a Namalenga ndikupemphera mwachikoka anamupezerela ali kunyumba ya nyakwawayo ali pa chikondi ndi mkazi wamwini yemwenso ndi membala wa mpingo wake. Anthu omwe anaona anthuwo akupita kunyumbako ndiwo anakatsina khutu mwamuna wa mkaziyo ndipo apa mwamunayo sanachedwe koma kulunjika kunyumba ya nyakwawayo ndi anthu ena adzitho. Apa mbusayo pamodzi ndi maiyo anaulura kuti kwa nthawi yayitali akhala akukomanilana kunyumba ya nyakwawayo. Anthu okwiya anayamba kuthambitsa makofi nyakwawayo, mbusayo pamodzi ndi maiyo uku akuwakokera ku bwalo la Mfumu ya ndondo. Ku bwaloko nyakwawayo inangoti kukamwa yasa kusowa cholankhula ndipo Mfumuyo inalamula nyakwawayo pamodzi ndi anthuwo kuti alipire mbuzi zingapo komanso nkukhu. Ku bwalo la Mfumu anthu onsewo anali olefuka chifukwa cha makofi ndipo mpakana anthu ena anawapaka matope. Kumapeto kwake Mfumuyo inachenjeza nyakwawayo kuti ikapitiliza ndi khalidwe lake lonyansalo alichotsa pa udindo pamene mbusayo anadzudzulidwa kwambiri kuti m’malo mosamala nkhosa za Ambuye m’malo mwake akutsogolera kuti anthu ambiri akathere ku moto wakujehena. Pakadali pano mbusayo ayamba amuimitsa pa ntchito yake yotumikira ntchito ya Ambuye ndipo wathawa mderalo.

Anthu asowa mosaziwika bwino ku Thyolo
Anthu ena asanu ndi m’modzi mdera la Mphuka mboma la Thyolo ati asowa mosadziwika bwino chifukwa cha uthakati. Nkhaniyi ikuti mpondamatiki wina mogwirizana ndi nyakwawa ya mderalo anaitanitsa Sing’anga wina kuti adzathane ndi mfiti zonse zomwe zakhala zikuvutitsa anthu a mderalo. Pa chifukwachi Sing’angayo atafika pa mudzipo anasilika nyumba ya mponda makwachayo ndipo patadutsa masiku awiri anthu mderalo anali odabwa atapeza kuti chinthu china chodabwitsa chomwe amakhulupilira kuti ndi ndege yauti anachipeza kutseri kwa nyumba ya Mkuluyo. Apa anthuwo mogwirizana ndi nyakwawa yao anapempha Sing’angayo kuti atembenuze chinthucho kuti anthu omwe anali mndegeyo adziwike pamene ena mwa anthuwo anapempha Sing’angayo kuti asatero ati kuopa kuti zidzetsa mpungwepungwe. Apa kusamvana kunabuka ndipo tsiku lotsatila anthu ena anasowa mosadziwika bwino. Pakadali pano sidzikudziwika kuti nkhaniyi yatha bwanji ndipo Nyakwawa ya mudzimo pamodzi ndi anthu ake akupitiliza kuumiliza Sing’angayo kuti aulure za athakatiwo.

Get Your Newsletter