26/04/17

Written by  Newsroom

Achilapa atagula nyama munjira
Mwamuna wina kwa Matenga m’boma la Ntchisi wanenetsa kuti sadzagulanso nyama iliyonse yongomutsatsa pa njira.

26
April

Nkhaniyi ikuti mderalo munthu wina anakadandaula ku gulu laza chitetezo kuti mbuzi yake sakuiona kwa masiku atatu ndipo pa chifukwachi gululo linatsimikizila bamboyo kuti amuthandiza kuyang’ana chifuyocho. Pa usiku wapa tsikulo mwa mwai anakomana ndi mwamunayo atasenza jumbo yomwe atafufuza bwino anapezamo matumbo komanso ziwalo zina za mkati mwa mbuzi. Apa anthuwo anakumbukira msanga za mbuzi yobedwa ija ndipo atamuthambitsa ndi mafunso mwamunayo anangoti kukamwa yasa kusowa choyankha koma pofuna kudzipulumutsa anaulura za komwe anagula nyamayo. Pa chifukwachi anatengerana ku maloko ndipo zinadziwika kuti mbuziyo ndiya bambo yemwe amadandaula uja. Pamene timalandila nkhaniyi nkuti yemwe anapezeka ndi jumbo ya nyamayo amukhululukira potengera kuti sanalakwepo komanso ngwa khalidwe labwino koma yemwe amagulitsa mbuziyo amukokera ku bwalo kuti akayankhe mlandu wakuba. Mwamuna yemwe wakhululukiridwayo wanenetsa kuti sadzayerekezanso kugula nyama yosadziwika bwino ngakhale ati iye ndiwa nkhwiru kwambiri.

Banja lina ligwidwa njakata
Banja lina mdera la Zulu ku Mchinji lagwira njakata chifukwa cha bokosi komanso nyama ya mbuzi yomwe anagula. Masiku apitawo mnyamata wapa khomopo yemwe amagwira ntchito yoyitanila maminibasi pa sitolo zapa Mchinji anamangidwa pomuganizila kuti anaphwanya malamulo . Chifukwa cha nkhaniyi mnyamatayo anamangidwa ndipo atampeza olakwa ku bwalo la milandu ndikumulamula kuti akakhale ku ndende kwa miyezi ingapo. Tsiku lina abale a mnyamatayo anapita koyendera mnyamatayo ku ndende koma mwachisoni anauzidwa kuti mnyamatayo wamwalira ndipo thupi lake liri ku nyumba ya chisoni koma chonsecho akuluakulu aku ndendewo anasemphanitsa za munthuyu poganizila kuti yemwe anamwalirayo anali mnyamatayo. Apa makolowo mwachangu anapita kunyumba ali okhumudwa ndipo apa ndi pamene anakapeza bokosi komanso chakudya choti anthu adye pa zovutazo kuphatikizapo nyama ya mbuzi. Tsiku lotsalita kuti akatenge zovuta anagwira kukamwa akuwapepesa kuti mwana waoyo ali moyo ndipo anawaitanila mpakana anacheza. Pamene timalandila nkhaniyi nkuti makolowo akusowa chochita ndi bokosi komanso chakudya chomwe anagula pa zovutazo. Anthu ena opemphera alangiza anafedwawo kuti zonse ndi zotheka ndi Ambuye choncho mkofunika kuzipempherela zinthuzo.

 

Alandidwa makadi aku banki
Anthu ena mdera la Chapananga manja ali ku nkhongo atawalanda makadi awo aku banki. Nkhaniyi ikuti anthu omwe ndi akuluakulu a gulu lina lokongozana ndikubwereketsana ndalama la banki nkhonde apezeka olakwa chifukwa chosokoneza ndalama za gululo. Izi zadziwika pamene gululo litafika kumapeto kwa nthawi yoti ligawane ndalama zao zoonjezera zotchedwa masheya. Koma chodabwitsa tsikulo litakwana akuluakuluwo anauza anthuwo kuti awadikirile kuti akatenge ndalamazo chonsecho akuzemba kuchita mantha chifukwa amadziwa kuti ndalamazo anali atazinyambita. Patadutsa sabata limodzi anthuwo anakamang’ala kwa mfumu ndipo apa anathandizana kuyang’ana anthuwo ndipo atawapeza anawakokera ku bwalo kuti ayankhe mlandu wosokoneza ndalama za gulu. Apa anthuwo sanapite patali koma kuulura kuti anasokoneza ndalamazo ndipo apa mfumu ya mderalo inalamula anthuwo kuti apereke ndalama zonsezo mwachangu apo bii akalowa mchitolokosi. Atamva zaku chitolokosi atsogoleriwo m’modzi m’modzi anapereka mabukhu awo aku banki kuti akatenge ndalama ina ili yonse gululo angakapeze ku ma akaunti awo. Pameme timalandila nkhaniyi mfumu ya mderalo yachenjeza anthuwo kuti ku makaunti awo akapanda kupezeka ndalama gululo ikanyamula katundu m’makomo mwao wolingana ndi kuchuluka kwa ndalamazo. Pakadali pano sidzikudziwika kuti nkhaniyi yatha bwanji chifukwa mwa zina anthuwo akuyenda monyowa kwambiri ngati nkhuku zogwera mvuwo.

Get Your Newsletter