25/04/17

Written by  Newsroom

Alanda mkazi wa chimwene

Mnyamata wina ku Mitundu m’boma la Lilongwe walanda mkazi wa mchimwene wake m’boma la Salima. 

25
April

Yemwe watumiza nkhaniziyi wati mnyamatayo wakhala ali pa banja ndi mkazi wina wa m’boma la Salima komwe anabereka mwana mmodzi. Koma chifukwa cha zovuta zina banjalo linatha ndipo  mkaziyo anabwerera kwao ku Salima. Tsono mwezi watha mnyamatayo adapita ku Salimako kuti akatenge mwana wakeyo. Koma atafika pakhomopo anadabwa kupeza mkulu wake weni- weni akutuluka mnyumba yake pamodzi ndi mkazi wakeyo. Ndipo atafunsa chomwe chimachitika anthu ena adamuudza kuti mwamunayo ndiye mwamuna wake wa mkaziyo watsopano. Apo anthuwo anasowa chochita atamva kuti amuna awiriwo ndi tuluka mtuluke ndipo kuti wamkuluyo walanda mkazi wa m’bale wake. Pakadali pano amuna awiriwo akuonana ndi diso lofiila.

 

Mnyamata opemphelera asekedwa

Mnyamata wina wopemphera  akumuseka ku Chilimba mu mzinda wa Blantyre. Yemwe watumiza nkhaniyi wati kumeneko  kuli mnyamata wina wodziwika mu mpingo wina  chifukwa chopempohera. Mwa zina iye amasala chakudya, kuthandiza anthu osowa, kuimba ndi mau anthetemya komanso kutumikira ku mpingo wake. Anthu akamufunsa pa zomwe iye wakhala akuchita iye amayankha mtima uli zii kuti  Mulungu amamuonetsera maso mphenya.  Ndipo miyezi itatu yapitayo mnyamatayo anauza mpingowo kuti anali ndi maso mphenya kuti apereke filiji yake kwa m’busa wa mpingowo kamba kuti Bible limati ali odala awo ali osauka popeza ufumu wakumwamba uli wawo. Izi zinachitikadi. Koma lamulungu lapitali mnyamatayo wadabwitsa mpingowo pomwe anaimilira pakati pa mapemphero kuti akufuna filiji yake. Koma m’bosayo pamodzi ndi akhirisitu ena adakana kuti sayenera kubweza filijiyo. Apo mnyamatayo sanaimve mpaka kukamang’ala nkhaniyi kwa nyakwawa mderalo kuti  m’busayo abweze katunduyo. Pakadali anthu akudikila ndi chidwi kuti amve kuti mfumuyo igamula bwanji nkhaniyi.

 

Azungulira mutu kamba ka mkazi

Mwamuna wina wazungulira mutu kamba ka mkazi pa estate ina kwa mfumu Kalumu m’boma la Ntchisi. Malinga ndi yemwe watumiza nkhaniyi wati pa estate ina pali mwamuna wina yemwe anali pa banja ndi mkazi wake yemwe banja lako loyamba linatha. Ndipo awiliwo pofuna kugonjetsa umphawi womwe wamanga nthenje pakati pao anapita pa estateyo kuti akagwire ntchito ya utenanti. Ngakhale mwamunayo amalimbika pantchito koma mkaziyo ndi manja lende, kamba safuna kugwira ntchito yolemetsa. Ndipo mkaziyo wakhala akuuza anthu kuti zinangovuta kuti anakwatiwa ndi mlimi wa fodya, iye anayenera kukwatiwa ndi chikhwaya osati akampota ngolo. Ngakhale amanena izi, mwamunayo analimbikabe kugwira ntchito pofguna kuti adzapeze ndalama zokwanira kuti adzaphe makwacha akagulitsa fodyayo. Koma mwezi dzana, mkaziyo wasiya mwamuna wakeyo ndikubwerera kwa mwamuna wake wakale kwa gulupu Chinkhwili m’boma la Dowa atamva kuti kumeneko mwamunayo ali pa mndanda wa anthu omwe akulandira thandizo la ndalama ndi zakudya kuchokera ku mabungwe othandiza anthu. Pakadali pano mlimiyo ati mutu wake sukugwira kamba wamuongera zambiri mkaziyo. 

 

Afuna kusamuka pa nsika 

Wamalonda wina akufuna kusamuka pa msika kwa Sadibwa mdera la Nkanda m’boma la Mulanje. Nkhaniyi ikuti masiku apitawo mkuluyo anatuma nzake kuti akagule katunda kwa wamalonda nzake pa msikawo koma pogwilitsa ndalama ya matsenga. Ndipo popeza wamalonda wianyo nayenso ndi katakwe pa zitsamba anatulukira kuti ndalama yomwe walandirayo inali yophika. Apo anaitembenuza ndalamayo  ndipo mwini ndalamayo anadziwa kuti madzi achita katondo. Zitatero mwini ndalamayo anakadandaula kwa akulu apamsikawo kuti wamalonda mzakeyo ndi wokhwima ndipo amubwezere ndalama yake yomwe akuitsunga. Koma wamalonda yemwe akutsunga ndlamayo wati nayenso apita ku Mozambique kwa ng’anga ina ya dzino limodzi yomwe amaitcha Kamano kuti athane ndi mzakeyo. Pakadali pano mwini ndalamyo wati achoka pamsikawo kamba kuchokera pomwe nkhaniyi inamveka mderalo makasitomala ake sakugulanso katundu mgolosale mwake ngakhalenso kumwa tea mu kantini yake.

Get Your Newsletter