16/03/17

Written by  Newsroom

Nyakwawa ithawa pa mudzi

Nyakwawa ina yathawa pa mudzi kusiya mudziwo opanda woutsogolera kwa Gulupu Muutcha mfumu Kachenga m’boma la Balaka.

16
March

Nkhaniyi ikuti mmudzimo muli nyakwawa ina yomwe inathamangitsa mkazi wake zaka zitatu zapitazo. Ndipo itatero inanyengerera mwana wa mchemwali wake kuti izigonana naye. Panthawi yomwe izi zimayamba nkuti mtsikanayo ali ndi zaka khumi ndi zisanu. Nyakwawayo inaopsyeza mtsikanayo kuti adzamupha ngati azaulutsa za ubwenzi wake ndi malume akewo. Koma masiku apitawo zadziwika kuti mtsikanayo yemwe ali ndi zaka 18 tsopano ali ndi pakati. Atampanikiza anaulula kuti pakatipo ndipa malume ake omwe ndi nyakwawa m’deralo. Apo achibale anakatula nkhaniyi kwa a gulupu ena mderalo kuti aweruze. Koma a gulupuwo atalandira nkhaniyi anaipondereza mpaka miyezi isanu ndi umodzi. Apo odandaulawo anakamang’alanso zankhaniyi ku polisi atadzindikira kuti a gulupuwo akulephera kuweruza nkhaniyo kamba ka sikono yomwe nyakwawayo inawapatsa powatseka a gulupuwo pakamwa komanso kuti aka sikoyamba kuti a gulupuwo apondereze nkhani ngati mderalo chifukwa cha ziphuphu. Apolisi sanachedwe koma kutsekela mchitokotsi nyakwawa ya upanduyo. Ndipo apolisiwo anatumanso uthenga kwa a gulupuwo kuti nawonso apite kupolisi kuti akakambe mbali yawo pankhaniyo. Koma a gulupuwo atamva za kuitanako apakila katundu wao yense ndi kusamuka mmudzimo pakati pa usiku. Moti ngakhale lamya yao ya mmanja sikupezeka anthu akayetsera kuimba. Pakadali pano, anthu awo ali ngati nkhosa zopanda m’busa.


Mwambo wa ukwati usokonekera

Mwambo wa ukwati usokonekera ku Mitundu mdera la mfumu yaikulu Chitseka m’boma la Lilongwe. Nkhaniyi ikuti masiku apitawo mderalo mudali mwambo wa ukwati. Koma pa zifukwa zina akuchimuna ndi akuchikazi anasiyana za dongosolo lonse la mwambowo. Mwa zina iwo anagwirizana kuti akatha kudalitsa ukwatiwo akuchikazi akachita madyerero kwa okha ndipo akuchimuna akadyera kwa okhanso. Ngakhale izi sizinakondweretse mkwati ndi mkwatibwi awiriwo anavomera kuti ukwatiwo uchitike monga anakonzera makolowo. Koma chomwe chachititsa kuti anthu agwedeze mutu wopanda mnyanga ndi choti tsiku lodalitsa ukwati litakwana akuchikazi sadafike kutchalichi komwe anakonza kuti ndiko adalitse ukwatiwo. Akuchimuna adazingwa pomwe adadikira pamalopo kwa maola atatu koma opanda akuchikazi. Koma momwe zimachitika izi nkuti ukwatiwo utamangidwa kale ku malo ena motsoghozedwa ndi akuchikazi okha. Ndipo akuchimuna atadzindikira kuti ukwatiwo wamangidwa kale ku malo ena, adathamangira kumaloko komwe anakwatula mkwatiyo. Koma apo akuchikazi anakwiya chifukwa cha zomwe akuchimunawo anachita ndipo mosakhalitsa ndeu inayamba pakati pa magulu awiriwo. Apo akuchimuna analandula kuti banjalo lathera pomwepo. Momwe nkhaniyi imatipeza nkuti chemwali ake a mkwatibwi atawatengera kuchipatala china mderalo chifukwa anakomoka kamba ka zomwe zinachitka pa tsikulo ndipo mkwatibwiyo sakudziwika komwe ali.

Deacon wina adabwisa anthu
Deacon wina wadabwitsa anthu pa mwambo wa ubusa kwa Gulupu Kaledzera kwa Mkhumba m’boma la Phalombe. Nkhaniyi ikuti mderalo muli mpingo wina womwe wakhala ukutengera anthu kuchipulumutso kamba kuti atsogoleri akewo ndi akhalidwe labwino. Koma monga malemba anena m’buku la Mateyu mutu 9 ndime 7 mpaka 8 kuti ntchito ilipo yambiri koma antchito ndi operewera, atsogoleri a mpingowo anakonza mwambo wodzoza ena mwa madeacon ake kukhala abusa. Athuwo akhala akuchita maphunziro kwa zaka ziwiri pofuna kuti akahale odziwa bwino ntchito yao. Limodzi mwa malamulo a mpingowo ndi loti munthu akhale ndi mkazi kapena mwamuna mmodzi. Koma chomwe chadadwitsa anthu mderalo ndi choti pa tsiku lo zodzoza ma deacon-yo mmodzi mwa wa iwo anabwera ndi akazi awiri. Ndipo pomwe anamuitana kuti amudzoze anaimilira pakati pa akazi awiri wina kumanzera komanso wina kumanja. Apo anthu anali odabwa popeza nthawi yomwe mnyamatayu amaphunzira komanso kupemphera kumpingowo sadanene kuti ali ndi akazi awiri. Atmufunsa iye chifukwa chomwe anabwera ndi akazi awiri pa mwambowo iye anati, AmbuyeYesu anapachikidwa pakati pa mbala ziwiri. Komabe ngakhale izi ndi zachilendo mu mpingowo, mkulu wa tchalichi-cho adadzozabe deacon-yo kukhala m’busa ndipo anati kuweruza ndi kwa mwini wake Mulungu. Koma ena mwa akhiristu mpingowo ati atuluka mu mpingowo popeza zomwe zachitikazo zikutsusana ndi zomwe Baibulo linena pa Genesis mutu 2 ndime 24 kuti mwamuna adzasiya makolo ake nakakwatira mkazi ndipo awiriwo osati atatu adzakhala thupi limodzi.

Get Your Newsletter