15/03/17

Written by  Newsroom

Buluzi asokoneza mwambo wa maliro

Mwambo wa maliro unasokonezeka kwa kanthawi pa mudzi wina kwa a group a Khoswe m’boma la Balaka buluzi atatsakamuka mu mtengo ku manda.

15
March

Nkhaniyi ikuti pa mudzipo panagwa zovuta za mkulu wina yemwe anthu akumuganizira kuti anali katakwe pa nkhani ya mankhwala a zitsamba. Mwambo wa zovuta pa siwa unayenda bwino lomwe mpaka ku manda. Nthawi yomwe adzukulu amatsitsira chitanda m’dzenje la manda chibuluzi chachikulu cha maonekedwe achilendo chinatsakamuka mu mtengo ndikumayenda m’mitu ya amai omwe anakhala pansi pa mtengo wa mango ku mandako. Amai onse anadzambatuka aliyense kuthawa ndipo mwambowo unasokonezeka kwa ka nthawi. Koma buluziyo anazimilira osaoneka komwe walowera. Ndipo nyakwawa yapa mudzipo inaimilira ndikuuza anthu kuti asadabwe kamba koti zimenezi zimachitika. Anthu ena ku malowo anadabwa malinga ndi zomwe inayankhula nyakwawayo. Ndipo nyakwawayo inapitiriza kuyankhula kuti akamva munthu wina akunena-nena nkhaniyi amulipitsa chindapusa.

 

 

Agululidwa mano awiri kamba kozithandiza pa sukulu ina

Mnayamata wina kwa Changoima kwa Chapananga m’boma la Chikwawa amugulula mano awiri komanso ina ikugwedera atampeza akudzithandiza pa chimbudzi chapa sukulu ina kumeneko. Watitumizira nkhaniyi wati m’nyamatayo yemwe amayendetsa njinga yamoto m’mimba mumvuta kotero kuti anaimika njinga yake mphepete mwa mseu pafupi ndi sukuluyo ndikuthamangira ku chimbudzi cha anyamata. Mlonda wapa malowo anangomuyang’ana, koma akutuluka m’chimbudzimo anamupha ndi mafunso, koma m’nyamatayo m’malo moyankhula modzichepetsa amayankha motumbwa kuti chimbudzichi ndicha ku nyumba kwako kunena mlondayo. Kamba ka izi mkangano unabuka pakati pa awiriwo , kotero kuti mlondayo anakuntha m’nyamatayo ndi ndodo kukamwa kotero kuti anamugulula mano awiri ndipo magazi anathoboka ngati amachokera pa mpope. Pamene anthu ena amadzaleletsa mkanganowo nkuti zovala za m’nyamatayo ziri magazi okha-okha. Ngakhale m’nyamatayo anakadandaula nkhaniyi kwa anyakwawa koma inamfera chifukwa mlondayo anakanena kuti munthuyo amafuna kukaba pa sukulupo.

 

 

Atuma galu kukaba zinthu

Mwamuna wina wokhwima wapa mudzi wa Kadamanja kwa Kafuzira m’boma la Nkhota-kota akumuloza-loza zitadziwika kuti wakhala akutuma galu wake kukaba zinthu za anthu m’makomo. Nkhaniyi ikuti mwamunayo yemwe chochita cheni-cheni sichidziwika, koma nthawi zonse pakhomo pake ndipa mwana alirenji. Tsiku lina galuyo anakazembetsa basket ya mai wina momwe munadzaza ndi zinthu zomwe anakagula ku msika. Maiyo atachokera ku msika anayedzeka basket-yo pakhonde iye ndikulowa m’nyumba. Koma galuyo yemwe sanadziwike komwe anachokera anakhwathula basket-yo ndikuthamanga nayo kulunjika kwa mbuye wake. M’basket-mo munali ndiwo za nkhuli, sugar, buledi komanso zinthu zina. Maiyo atatuluka panja anadabwa mpaka kuzungulira nyumba yake kangapo konse akufuna-funa basket-yo koma sanaipeze. Maiyo anatsala pang’ono kugwetsa msozi poganizira kuti ndalama zina azipeza kuti zoti akagulire zinthu zina zapa banjapo, komanso ayankhulanji kwa mwamuna wake. Atakweza maso ku mseu anaona basket yake iri mphepete mwa mseu koma mulibe kanthu. Maiyo akupukusa mutu wopanda nyanga poganizira kuti izi zimachitika nkanthawi kochepa kwambiri. Pakadalipano mbiri yawanda pa mudzipo kuti mkuluyo ndi yemwe akuliza anthu pomatuma galu wake m’matsenga yemwe
akumabera anthu.

Get Your Newsletter