14/03/17

Written by  Newsroom

Akanganilana mitengo yaku manda
M’nyamata wapa mudzi wina kwa Chanthunya m’boma la Balaka wakangana kwambiri ndi mai ake polimbirana mitengo yaku manda.

14
March

Nkhaniyi ikuti m’nyamatayo yemwe ndi waku banja lachifumu masiku apitawa amafuna kukadula mitengo ku manda apa mudzipo n’cholinga choti atenthe makala. Koma mai ake a m’nyamatayo omwe ndi namfedwa chifukwa choti amuna awo omwe ndi nyakwawa yapa mudzi wina m’bomalo anatisiya masiku apitawa. Phokoso linakula pakati pa m’nyamatayo ndi mai ake kotero kuti anthu ena ndiwo analeletsa mkanganowo. Koma m’nyamatayo amanenetsa kuti palibe munthu yemwe angamuletse kudula mitengo yaku mandayo chifukwa chakuti iye ndi amene akhale nyakwawa yapa mudzipo masiku akudzawa. Anthu ambiri kuphatikizapo mikoko yogona yati nkofunika kuti anthu aganize kawiri pamene akufuna kusankha munthu woti alowe unyakwawa pa mudzipo, chifukwa m’nyamatayo waonetseratu kuti ndi woononga.

 

 

Mkulu wina wadzitsamba achenjezedwa

Mwamuna wina yemwe ndi katakwe pa mankhwala a zitsamba kwa Khuwi m’boma la Ntchisi amuopsyeza kuti akapitiriza kuchita zamatsenga zakezo aona chomwe chidameta nkhanga mpala. Achibalewo aopsyeza mwamunayo kamba ka zomwe wachita masiku apitawa pakupha mwana wake wa mtsikana m’matsenga. Nkhaniyi ikuti mwana wa mkuluyo anali ndi pakati , kotero kuti nthawi yake yochembeza itakwana anakabereka ku chipatala. Koma zodabwitsa nzakuti khandalo litakwanitsa masiku 27 mai ake anamwalira mosadziwika bwino. Mai a khandalo amadandaula kuti mutu umamupweteka mpaka kutsikira nawo kuli chete. Anthu ambiri , makamaka achibale a mkulu wokhwimayo anenetsa kuti akudziwa kuti mtsikana wochembezayo anamukong’ontha ndi hamala. Achibale a munthu wokhwimayo aopsyeza kuti aponda-ponda ndipo zomwe apeze abwezera kwa mkuluyo kuti nayenso aone chomwe chidameta nkhanga mpala.

 

Wamisala asokoneza malonda
Malonda anasokonezeka pa msika wapa boma la Mchinji wamisala wina atayamba kuyendetsa minibus yomwe dalaivala wina anaimitsa mu depoti ya bus m’bomalo. Nkhaniyi ikuti m’nyamata wina yemwenso anali dalaivala wa minibus m’buyomu wakhala akusuta chamba zomwe makolo ndi achinansi amamuletsa koma malangizowa amatulukira ku nkhongo. Makolo ndi anansiwo akhala akumuuza kuti akapitiriza khalidweli apenga kamba ka chambacho. Koma iye nthawi zonse wakhala akuyankha anthuwo kuti akupengawo chifukwa cha chamba ndi a mitu yaingono. Koma miyezi yapitayi anthu anadabwa malinga ndi momwe m’nyamatayo amayendetsera minibus zomwe zinachititsa kuti bwana wake amuchotse ntchito. Ndipo anthu anadabwa masiku apitawa kuti m’nyamatayo anayamba kutoleza zitsipe za nzimbe mpaka achibale kuchita kumuveka zovala, atavula kukhala mbulanda. Misalayo inafika pokhodzokera atapita ku chipatala cha anthu a misala ku Zomba koma anabwerako chimodzi-modzi. Ndipo wamisalayo tsiku lina atakafika ku kwao m’boma la Mchinji amayenda kufupi ndi depo ya bus. Ndipo anapeza minibus ina yomwe dalaivala wake anasiya makiyi momwemo. Mosakhalitsa wamisalayo anayendetsa minibus-yo mothamangitsa kwambiri kotero kuti anthu ena amachita kuthawitsa minibus ndi galimoto zawo kuopa kuti angaziombe. Madalaivala ena amamutsatira wamisalayo pa galimoto zawo , ndipo mwa mwai minibus-yo inazima itatha mafuta. Ndipo anthuwo anamutulutsa m’minibus-yo uku ena akumukuntha mosamvera chisoni. Pakadalipano dalaivala wa minibus-yo sakumvetsa kuti kodi zikanatha bwanji kwa bwana wake.

Get Your Newsletter