13/03/17

Written by  Newsroom

Chidakwa china chikunthidwa pofunsira mkazi wa mwini

Chidakwa china chapa mudzi wa Phazi kwa Chadza m’boma la Lilongwe chiri mu ululu wopsya mwini mkazi yemwe anamfunsira chibwenzi atamukuntha ndikumugulula mano awiri.

13
March

Watitumizira nkhaniyi wati mwamuna wina wa mitala pa mudzipo , tsiku lina anali kwa mkazi wake wamkulu. Ndipo mkazi wake wang’ono amacheza kachasu. Tsiku lina nkachisisila mwamunayo anakafika ku nyumba ya mkazi wake wachiwiriyo. Uku anakapeza makasitomala akupapira bibida. Chidakwa china chomwe chinaona mwini mkaziyo sichinazindikire kuti ndiye mwini khomo koma amaganiza kuti ndi m’modzi mwa makasitomala wodzagula mowa. Chidakwacho chitaitanitsa velemoti chinayankhula mocheza kwa mkazi wogulitsa mowayo kuti akumufuna ubwenzi. Mwini mkaziyo atamva mauwa anadzambatuka ndikukuntha chidakwacho mpaka kumugulula mano awiri. Anthu ena achifundo anatengera chidakwacho ku chipatala komwe chinakalandira thandizo la mankhwala. Anthu ambiri pa mudzipo akudzudzula mwini mkaziyo kamba ka khalidwe lomwe anaonetsalo, ena akuti n’chifukwa chiyani sanaletse mkazi wakeyo kuti asamacheze kachasu.

 

 

Aonetsedwa zakuda pozembelerana ndi mamuna wa mwini

Mkazi wina kwa Kankao kwa Chanthunya m’boma la Balaka amuonetsa mazangazime kamba kozemberana ndi mwamuna wa mwini. Nkhaniyi ikuti mkazi wina yemwe ndi mbeta pa mudzipo wakhala akuzemberana ndi mwamuna wa mwini. Mwini mwamunayo atatulukira kuti mwamuna wake akumudyetsa njomba pozemberana ndi mkazi wina anakungana ndi achibale ake komanso anthu ena akufuna kwabwino. Tsiku lina pamene anthu pa mudzipo amakalandira thandizo la chimanga mwini mwamunayo pamodzi ndi achibale ake anamuonera patali mkazi wakubayo kotero kuti anamuwakha ndikumukuntha mosamvera chisoni. Anthu ena omwe anali pa malowo ndi omwe analeletsa nkhondoyo. Koma pamene amaleletsa nkhondoyo nkuti zovala za mkazi wakuba ziri nsanza zokha-zokha. Pakadalipano mkazi wakubayo akubindikira m’nyumba kamba koti mbiri yake yawanda m’deralo.

 

 

Mwamuna wina wamchiuno athawira kwao

Mwamuna wina wa mchiuno yemwe amakhala pamudzi wa Msaka m’boma la Balaka wathawira kwao m’boma la Mwanza mphepo itampeza kuti mwini mkazi yemwe amazemberana naye akumufuna-funa kuti amuonetse chomwe chidameta nkhanga mpala. Nkhaniyi ikuti mwamunayo anasamukira m’boma la Balaka chaka chapitachi komwe wakhala akuchita geni. Ngakhale kuti mwamuna wa geniyo ndi wapa banja koma samaphetira akaona akazi a eni. Zomwe zinachititsa kuti tsiku lina aponye mau kwa mkazi wina wapa banja mpaka ubwenzi wa awiriwo kufumbira. Mkazi wapa banjayo amafera ndalama zomwe mwamuna wa bizinesiyo amamupatsa zomwe amagulira zofuna zake. Mwamuna wake akamufunsa kuti ndalama zomwe amagulira zinthuzo amazitenga kuti, iye amanamiza mwamunayo kuti amapeza malinga ndi maganyu omwe amagwira. Koma tsiku lina anthu ena anapezelera mwamuna wa bizinesiyo ali pachikondi ndi mkazi wa mwiniyo. Mwamuna wa bizinesiyo anathawa ndipo atakafika ku nyumba anakatsazika mkazi wake kuti akubwelera ku mudzi kwao ku Mwanza ndipo anamusiira ndalama mkaziyo kuti amutsatire. Mwamuna wa bizinesiyo anapitiriza kuuza mkazi wakeyo kuti bizinesi sikuyenda bwino ku Balaka-ko ndipo akapitiriza ku mudzi kwao. Mwini mkazi yemwe amazemberana ndi mwamuna wa bizinesiyo analawilira kwa mwamuna m’nzakeyo kuti akamphike koma sanampeze. Apa mpamene mkazi wa mwamuna wa bizinesi anadziwa choonadi chomwe mwamuna wake wathawira ku Balaka.

Get Your Newsletter