12/03/17

Written by  Newsroom

Nyakwawa itolera ndalama kunamizira mfumu

Anthu mdera lina kwa Masaula m’boma la Zomba ati ndi okhumudwa ndi khalidwe la nyakwawa ina yotolera ndalama ponamizira mfumu yaikulu.

12
March

Chomwe chinachitika mchoti mfumu yaikulu mderalo inaitanitsa msokhano ndikuchenjeza makolo kuti adzilipila ndalama ngati mwana wao apezeka atasiila sukulu pa njira kamba ka ukwati. Ndipo tsiku lina nyakwawa ina inatolela chindapusa cha ndalama zokwana 30-thousand kwacha kwa makolo angapo mderalo omwe ana ao ali ndi pathupi ndipo asiya sukulu ndikunamiza makolo a anao kuti ndalamazo akazitula kwa mfumu yaikulu mderalo. Koma atafika ku nyumba nyakwawayo inangoti duu ndikuyamba kutsakaza ndalamazo m’malo mokapereka kwa mfumu yaikuluyo. Koma mphuno salota m’mudzimo munachitika zovuta ndipo m’modzi mwa anafedwa anakagwada kwa mfumu yayikulu yomwe inali pa maliropo ndikudandaula kuti nyakwawa ya m’mudzimo siyinabweze chenje cha ndalama zokwana 5-Hundred Kwacha zomwe anatenga ku banjako ngati chindaputsa kamba ka zomwe anachita mwana wake wa mkazi potenga pathupi ndikusiya sukulu panjira. Apa mfumu yaikuluyo inadzidzidzimuka ndi nkhaniyi ndipo inaitanitsa nyakwawa yomwe inakatolera ndalamayo. Nkhaniyi itafika kwa nyakwawa yaukathyaliyo, inangoti ndwiii ndipo podziwa kuti madzi achita katondo, mkuluyu anathawa mpaka pano sakudziwika komwe walowera. Pakadali pano mikoko yogona yati ikumana kuti isankhe munthu oti adzigwira ntchito za nyakwawayo ndipo akumudikira kuti nyakwawayo ikadzabwera idzayakhe mlandu wakuba ndalama mwachinyengo.

 

M'busa wina akakamila pa malo

M’busa wa mpingo wina ku Mangochi-Turn Off ku Liwonde watemetsa nkhwangwa pa mwala ndipo wanenetsa kuti zivute zitani sachoka pa malo omwe akutumikilapo. Chomwe chachitika mchoti m’busayo alandila kalata kuchokera ku likulu la mpingowo yomutuza kuti akatumikire ku malo ena. Nkhaniyi itafika kwa akulu akulu a mpingo pa malopo analengeza ku chalitchi ndipo anthu anasonkherana ndalama zotsazikana ndi m’busayo. Koma tsiku litakwana akulikulu la mpingowo anatumiza m’mbusa wina kuchokera ku Mangochi ndipo atafika pa chalichicho, anthu anakhumudwa kuti nyumba yomwe amayembekeza kuti alowe ikadali yokhoma mpaka pano. Anthu osatila mpingowo kuphatikiza akulu akulu ampingo anayetsa kuyimbila lamya m’’busa yemwe amayembekezeka kusamukayo koma siimagwira. Zikumveka kuti m’busayo anasiya kalata pa khonde yonena kuti iye satuluka mnyumbamo ngakhale akulikuluwo akumutsamutsa pa malopo. Pakadali pano katundu wa m’mbutsa watsopanoyo wangokhala mgalimoto ndipo anthu ena achifundo asokherana zakudya kuti m’busa watsopanoyo adye pamene akuyembekezera winayo kuti achoke pa malopo.

 

 

Mai wina asokoneza ntchito pa chipatala
Mai wina wasokoneza ntchito pa chipatala china ku Milepa mdera la Mulanje North m’boma la Mulanje. Yemwe watumiza nkhaniyi wati mderalo mudafika banja lina kuchokera m’boma la Rumphi komwe limagwira ntchito yolima fodya pa esiteti ina kumeneko. Banjalo lomwe lili ndi mwana mmodzi wa miyezi isanu ndi umodzi linali la chitsanzo popeza anthu amaliyamika chifukwa cha khama lake pa ntchito komanso chuma chomwe apeza atagwira ntchito yolima fodyayo. Koma banjalo litafika mderalo mwamuna adayamba kuzembera mkazi wake pomwe wapeza mkazi wina yemwe akudya naye makobiri mdera lomwelo. Kanthawi yaitali mkazi wa mwamunayo samadziwa chili chonse mpaka dzana Lolemba pomwe zadziwika kuti mwamunayo ali ndi chibwenzi cha mseli. Yemwe watumiza nkhaniyi wati Lamulungu tsabata ino mwamunayo anatsanzika mkazi wake kuti akupita ku Chambe kukayendera amalume ake. Apo njondayo inapopa njinga yake ndichoka pakhomopo ulendo wopita kuchibwenzi ndipo anagona komweko. Mmawa kutacha njondayo ndi mkazi wakubayo anapita kuchipatala china mderalo kuti akayezetse magazi ku kachilombo ka HIV. Mphuno salota nayenso mwini mwamuna tsiku lomwelo anapitanso ku chipatalako kuti akapeze njira zolera. Ali kuchipatalako anadabwa kuona njinga ya mwamuna wake ili pa khoma komanso mwamuna wake atakolekana mikono ndi mkazi wa chilendo. Apo mwini mwamunayo sanaimve ndipo anamangira msalu mu mchuno ndikugwira mkazi nzakeyo pakhosi. Awiriwo anayamba kutuwitsana ndi zibakera komabe wakubayo amachepera kaba moti panthawi yomwe anthu amaleletsa ndeuyo nkuti mkazi wakubayo ali magazi okhaokha.

Get Your Newsletter