09/03/17

Written by  Newsroom

Azembelana ndi mkazi wamasiye
Mwamuna wapa mudzi wina kwa Chiwalo m’boma la Phalombe akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi mbiri itawanda kuti akuzemberana ndi mkazi wina wamasiye pa mudzipo.

09
March

Nkhaniyi ikuti mwamunayo yemwe ndi wodziwika bwino komanso ali pa banja lolozeka wakhala akuzemberana ndi mkazi wamasiyeyo. Mkaziyo yemwe akukhala kwa makolo ake pa mudzipo wakhala akuyenda mwa nseri ndi mwamunayo. Mwini mwamunayo mbiri itampeza anakachita nkhondo ku banja la mkazi wamasiyeyo. Pakadalipano, mwamunayo akubindikira m’nyumba atazindikira kuti mbiri yake yawanda pa mudzipo. Ndipo naye mkazi wamasiyeyo wathawira ku tauni kwa m’ngono wake kukapitidwa mphepo.

 

Atenga mulamu kukhala mkazi wachiwiri

Anthu ena apa mudzi wa Mbirizi kwa Mlauli m’boma la Neno akuchita njiru ndi mwamuna wina wa bizinesi yemwe waphatikiza mlamu wake kukhala mkazi wake wachiwiri. Nkhaniyi ikuti mwamunayo ndi wodzilimbikira kotero kuti amachita bizinesi pa mudzipo. Zaka zapitazi atafunsira mbeta ku banja lina mkaziyo anamutenga nkumakhala naye pa mudzi pomwepo. Kuyambira nthawiyo mkazi wake anakatenga m’ng’ono wake nkumakhala naye pakhomopo. Kotero kuti mtsikanayo waphunzira sukulu akukhala ndi mkulu wakeyo. Koma anthu masiku apitawa adabwa kuti munthu wabizinesiyo wamangira nyumba mlamu wakeyo pa mudzi pomwepo kukhala mkazi wake wachiwiri. Pakadalipano mkazi wachiwiriyo ali ndi khanda. Koma chodabwitsa nchakuti makolo ndi ankhoswe akungoyang’ana poganizira kuti mkamwiniyo waathandiza potenga mtsikanayo kukhala mkazi wake wachiwiri.

 

Adzukulu afuna kulipilidwa ndi anamfedwa

Adzukulu ena apa mudzi wa Midu m’boma la Salima anaseketsa anthu atayankhula m’maso muli gwa kuti akufuna anamfedwa awalipire kamba ka ntchito yomwe anagwira yosema mipini ya makasu. Nkhaniyi ikuti ku banja lina pa mudzipo kunagwa zovuta, kotero kuti adzukulu monga mwa nthawi zonse anakagwira ntchito yawo ku manda. Koma akugwira ntchitoyo mipini ya makasu inathyoka malinga ndi dothi la katondo. Kamba ka izi adzukuluwo anadula mitengo ina ku mandako ndikusema mipini ina yomwe anakhomera makasuwo ndikupitiriza ntchitoyo. Pomaliza adzukuluwo analamula anamfedwa kuti awalipire malinga ndi ntchito yosema mipini yomwe anagwira. Nkhaniyi inakafika ku bwalo la anyakwawa kamba koti anamfedwawo analibe ndalama zolipira adzukuluwo. Ku bwalo la anyakwawa adzukuluwo anawapanikiza ndi mafunso kuti ulamuliro wolipiritsa ananfedwa autenga kuti. Adzukuluwo anayesera kuyankhapo koma m’malo mwake nyakwawa inalamula adzukuluwo kuti alipire chindapusa kamba kopeputsa maliro.

Get Your Newsletter