08/03/17

Written by  Newsroom

Azukulu asemphana maganizo ndi mikoko yogona

Adzukulu okumba manda anasiyana nzeru ndi mikoko yogona pa nthawi yoikira maliro kwa Kalolo m’boma la Lilongwe. Nkhaniyi ikuti masiku apitawo mmudzi wina mderalo munagwa maliro.

08
March

Ndipo mmawa kutacha adzukulu anatengqa makasu kukagwira ntchito yokumba manda. Ntchitoyo itatha adzukuluwo anatumiza uthenga kusiwa kudziwitsa mafumu ndi nduna zao kuti ntchito yokumba manda yatha. Koma mafumuwo anaudza adzukuluwo kuti abadikira kaye kamba panali zina zoti achite pasiwapo koma sanamasule chomwe mafumuwo amatanthauza. Izi zinakwitsa adzukuluwo kamba zimatsusana ndi malamulo oikila maliro omwe anthu motsogozedwa ndi mafumuwo mderalo anagwirizana. Mwa zina lamulolo limati maliro amwana aikidwe isanakwane 12 koloko ndipo a mkulu isanakwane 2 koloko masana. Adzukuluwo ataona kuti 2 koloko yadutsa anafika pasiwapo ndikutenga malirowo opanda kukambirana ndi mafumu zankhaniyo. Anthu omwe anali pasiwapo ena anaombela mmanja adzukuluwo kamba kolimba mtima kutenga malirowo. Ndipo zadziwika kuti mafumuwo analephera kutulutsa chitanda motsatira dongotsolo kamba kadyera popeza panthawi yomwe adzukuluwo amafika pasiwapo mafumu anali asanadye.

 

 

Gule asokoneza mwambo wa chiliza

Gule wotchedwa Pinimbira lero wasokoneza mwambo wa chiliza kwa Kalonga m’boma la Salima. Nkhaniyi ikuti lero mderalo munali mwambo wachiliza cha mkuklu wina yemwe anamwalira zaka ziwiri zapitazo. Yemwe watumiza nkhaniyi watinso omwalirayo anameta kutanthauza kuti anali wa gule ndipo mwambo wamaliro ake panthawiyo, anayendetsa ndi agule. Koma chomwe chadzutsa mapiri pachigwa ndi choti pomwe amachita mwambo wachiliza lero abale ake anaitana a fellow-ship kudzayendetsa mwambowo. Izi zinakwitsa anthu agule mderalo. Ndipo anthu ali paulendo wakumanda kukaona chiliza mwadzidzidzi pamalopo panafika gule yemwe amadziwika kuti Pinimbira ndikubalalitsa anthu pamalopo ndipo mwambowo unathera pomwepo. Pakadali pano, anthu mderalo akudikira ndi chidwi kuti aone momwe nyakwawa ya deralo iweruzire nkhaniyi.

 

Adyerana masuku pamutu

Anyamata ena apachinzake adyerana masuku pamutu mmudzi wa Mapanganya mdera la Themba la Mathemba Chikulamayembe mdoma la Rumphi. Nkhaniyi ikuti patsikulo anyamata awiri omwe amacheza kwambiri limodzi anatengana kupita kudimba komwe awiriwo alima mbeu zakudimba. Koma ali kudimbako mmodzi wa anyamatawo anatsanzika mnzake kuti wadwala ndipo akubwerera kunyumba. Koma pochoka kudimbako anayendera kunyumba ya mzake komwe ananyengerera mkazi wa mzakeyo mpaka kuchita naye zadama. Ndipo awiriwo ali mkati mogawana chikondi mwini nyumbayo yemwe anatsala kudimba uja anafika pakhomopo. Apo mwini nyumbayo anadabwa pomwe anapeza mzake weni weni yemwe anali naye kudimba ali mbulanda ndi mkazi wake pakama. Anthu mderalo akuganiza kuti chibwenzi cha anthu awiriwo ndichamgona-gona. Pakadali pano mwamuna wakubayo wasowa mderalo ndipo sakudziwika komwe ali.

Get Your Newsletter