02/03/17

Written by  Newsroom

Akunthana kamba ka mbewa

Anyamata atatu akwa Khombe kwa Chadza m’boma la Lilongwe anakunthana koopsya polimbirana mbewa za m’dzinja.

02
March

Watitumizira nkhaniyi wati anyamatawo anakachera zigolo-golo misampha inde yophera mbewa m’zithukuluzi zaku famu ina ku Bunda m’deralo. Ndipo kutacha m’mawa anyamatawo anakaonjola misamphayo kotero kuti anakola mbewa za mtundu wa thini ndi zina zomwe zimapezeka dzinja lino m’zithukuluzi komanso mu khonje. Koma m’mawa kutacha m’modzi mwa anyamatawo analawilira kukaonjola umodzi mwa misamphayo mozembera anzake. Zigolo-golozo inde misamphayo inakola mbewa zambiri. Ndipo anzake atatulukira ku malowo anapeza msmpha umodzi palibe koma inatsa iwiri yokha. Apo anyamata enawo anadziwiratu kuti m’nzawoyo ndiye waadyetsa njomba. Atakafika ku mudzi mkangano unabuka pakati pa anyamata awiriwo ndi m’nzawo yemwe anaonjola msamphayo pa yekha. Mkanganowo utakula nkhaniyi inakafika kwa anyakwawa omwe akuyembekeza kuweruza nkhaniyi masiku akudzawa.

 

 

Afunsira mkazi wa mzake
Amuna awiri a bizinesi pa msika waku Kapiri m’boma la Mchinji akunthana koopsya wina atafunsira mkazi wa m’nzake. Watitumizira nkhaniyi wati amuna a bizinesiwo ali moyang’anizana mu msikawo pamene wina amagulitsa zipangizo za hardware pamene winayo amagulitsa mapepala a pulastic. Tsiku lina mwamuna wogulitsa katundu wa hardware-yo anafunsira mkazi wa m’nzake atakomana naye pa njira. Mwamuna wa bizinesiyo anayankhula zambiri kuphatikizapo kunyoza mwamuna m’nzakeyo yemwe ndi mwini mkazi. Mkaziyo sanachitire mwina koma anakafotokozera nkhaniyi mwamuna wake. Naye mwini mkaziyo sanaugwire mtima koma m’malo mwake anathamangira kwa mwamuna m’nzakeyo mtima uli mwamba. Uko anakafikira kusama pakhosi m’nzakeyo uku akumfunsa kuti umandidyetsa ndi iwe?Bwanji umafunsira mkazi wanga? Amuna awiriwo anagwirana pa msikapo mpaka anthu analeletsa mkanganowo. Koma nthawi yomwe anthu amaleletsa nkhondoyo n’kuti malaya a mwamuna wa hardware-yo ali nsanza zokha-zokha komanso atamugulula mano awiri. Uku amuna awiriwo akupumira mwamba monga muja achitira atambala atautsirana chenjelere. Pamene timalandira nkhaniyi nkuti mwamuna wa Hardware-yo akupita kukadandaula ku polisi komanso kukatenga chikalata choti akalanndire thanndizo la mankhwala ku chipatala.

 

 

Akunthidwa mpaka kukozedwa

Mnyamata wina yemwe amatchuka ndi dzina lakuti NIJO kwa Ndindi m’boma la Salima anamukuntha kodetsa nkhawa mpaka mkodzo wa!wa!wa!. Mnyamatayo yemwe amadzitama kuti ndi wotchuka chifukwa akafunsira akazi samukana anaona ngati malodza masiku apitawa anthu ena mderalo atamududuluzira kwa anyakwawa. Anthuwo ati anachita izi chifukwa mnyamatayo mwa zina wakhala akutenga ndalama za weni komanso paza khalidwe lake la nchiuuno. Pa tsikulo anyamata amzake anamuimitsa mzaoyo ali pa njinga koma iye anayankhula mwa thamo kuti sangatsike pa benzi yake zomwe zinakwiyitsa anyamatawo mpakana kumugwetsa pansi uku akumuthidzimula mpakana kukodzedwa. Mnyamatayo anachonderela anzakewo kuti amukhululukire ndiponso kuti waleka paza khalidwe lake loipalo. Apa anthuwo anagwirizana zomusiya mzaoyo koma anamuchenjeza kuti alekeretu paza khalidwe lakelo chifukwa akapitiriza adzaona chomwe chidameta nkhanga mpala. Anthu ambiri makamaka achinyamata akuseka mnyamatayo. Pamene timalandila nkhaniyi nkuti mnyamatayo atamulanda njinga yake yakapalasa . Pakadalipano m’nymatayo kubindikira mnyumba chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.

 

Get Your Newsletter