28/02/17

Written by  Newsroom

Amanga banja ndi wantchito wawo
Mai wina wapa mudzi wa Madyelatu kwa Chanthunya m’boma la Balaka wadabwitsa anthu atamanga banja ndi wa ntchito wake wolima m’munda.

28
February

Nkhaniyi ikuti maiyu yemwe ali ndi zaka pafupi-fupi 45 wakhala pa banja ndi mwamuna wina wa geni yopha nkhumba kwa zaka zambiri. Pa zifukwa za m’banja mkaziyo anasiyana ukwati ndi mwamuna wake. Mwamunayo anaola katundu wake ndikuona msana wa njira. Mkaziyo atatsala pakhomopo anangoti pasavute ananyengelera m’nyamata wao wolima ku munda wa zaka 21 kuti akwatirane. M’nyamatayo poona momwe paliri pakhomopo anangoti laponda la mphawi, iye anagwirizana ndi malingaliro a mkaziyo. Ngakhale mbiri yawanda m’deralo malinga ndi zomwe maiyo wachita pokwatiwa ndi wa ntchito wake wolima ku munda. Koma maiyo sizikumukhudza ndipo akukhalira kunena kuti amene ziwapweteke ndi owonelerawo.

 

Mkazi akuntha mamuna wake kamba ka mitala

Mkazi wina wa dzitho wapa mudzi wa Maiton m’boma la Balaka wapanilira ndikukuntha mwamuna wake pamene mwamunayo amakakamira kukwatira mitala.Nkhaniyi ikuti banjalo lakhala loopa Chauta kotero kuti linali la chitsanzo kwa ena. Nthawi zambiri mkazi ndi mwamunayo akhala akutsagana ku mapemphero. Koma masiku apitawa mkaziyo wakhala akudabwa ndi mayendedwe a mwamuna wake pomwe samapita ku mpingo. Atampanikiza ndi mafunso mwamunayo anayankha m’maso muli gwa kuti wakayamba ku ku mpingo wina m’boma la Ntcheu. Izi zimachitika chifukwa pa mudzi pomwe awiriwo akukhala uli m’malire a boma la Balaka ndi Ntcheu. Koma mkaziyo atachita kafuku-fuku wake wapeza kuti mwamunayo akutsatira ku mpingoko mkazi wina yemwe wapalana naye ubwenzi wa nseri. Ndipo tsiku lina mwamunayo anayankhula m’maso muli gwa!!! kuti ndi zoona wapeza mkazi wina kuti akwatire mitala. Izi zinakwiitsa kwambiri mwini mwamunayo mpaka phokoso kukula m’banjalo. Ndipo mwamunayo amafuna kutenga thumba la nandolo ndi chimanga mozembera mkazi wamkuluyo kuti azikadya kwa mkazi wa m’ng’onoyo. Mkanganowo unakafika kwa ankhoswe omwe akudikira kukambirana nkhaniyi masiku akudzawa. Pakadalipano mwamunayo akukhala kwa mkazi wa m’ng’onoyo, ndipo wanenetsa kuti sasiyana naye.

 

Chidakwa china chilandidwa mkazi
Chidakwa china pa mudzi wa Mazinga kwa Chiseka m’boma la Lilongwe chikubindikira m’nyumba misozi ikutsikira m’mimba kulira mkazi wake yemwe mwamuna wina wamulanda.Watitumizira nkhaniyi wati chidakwacho chiri ndi chizolowezi chokhala chiledzelere kotero kuti ntchito zapa khomo amagwira ndi mkazi. Mkaziyo potopa izi tsiku lina mwamuna wina atamponyera mau achikondi anagonekera khosi ndikulola ubwenziwo. Ubwenzi wa awiriwo utafumbira awiriwo amakomana ku nyumba kwa mkaziyo pa nthawi yomwe mwamuna wakeyo amakhala akupapira bibida. Koma tsiku lina chidakwacho chinapezera mwamuna wakubayo ali pa chikondi ndi mkazi wake m’nyumba. Koma chidakwacho chinalephera kulimbana mokwanira ndi mwamuna wakubayo, mpaka anapeza mpata wothawa. Ndipo mwamuna wakubayo atathawa anazungulira khonde ndikubisala kuseri kwa nyumba kudikilira mkaziyo.Mosakhalitsa chidakwacho chinayamba kuliza mkonono pomwe chinakhala. Mkaziyo anabereka mwana wake kumbuyo ndikulongedza katundu wake kuthawa kusiya chidakwacho chikuliza mkonono m’nyumbamo. Pakadalipano, chidakwacho chamva kuti mkazi wakeyo akukhala ndi mwamuna wakubayo pa mudzi wina m’deralo. Ndipo watuma atsibweni ake kuti akagwire mwendo kwa mkaziyo.

Get Your Newsletter