27/02/17

Written by  Newsroom

Afuna kukunthidwa ku manda 

Mkulu wina wapa mudzi wa Mbunumbu kwa Mkanda m’boma la Mulanje akuyenda wera-wera ngati wataya singano adzukulu wokumba manda atatsala pang’ono kumukuntha ku manda.

27
February

Nkhaniyi ikuti mkuluyo yemwe ndi wodziwika bwino pa mudzipo kamba ka ntchito zake zothandiza kukagwa zovuta pa mudzipo. Tsiku lina kunagwa zovuta ku banja lina pa mudzipo, ndipo mkuluyo anadzipatsa udindo wa usabwira. Adzukulu akugwira ntchito yawo ku manda mkuluyo anathmangira komweko, komwe modabwitsa adzukuluwo mkuluyo mosagwirizana ndi aliyense anayamba kumatenga dothi lochokera m’dzenjelo nkumalipititsa mbali ina ya dzenjelo. Adzukuluwo atamfunsa mkuluyo anayankha zokhadzula nkumati iye ndi msabwira ndipo adzukuluwo alakwitsa pa momwe adaponyera dothi la m’dzenjelo. Adzukuluwo anazunguzika mitu malinga ndi zomwe amachita mkuluyo kamba koti kwa iwo zomwe amachita mkuluyo ndi zachilendo kotero kuti anatsala pang’ono kumukuntha koma anthu ena omwe anali ku mandako ndi omwe analeletsa mkanganowo. Anamfedwa atamva nkhaniyi anakhumudwa kwambiri malinga nkuti sanamutume mkuluyo kuti akachite zomwe amachitazo ku manda. Pakadalipano mkuluyo akuyenda mogwetsa nkhope yake pansi kamba koti nkhaniyi yawanda m’deralo.

 

Mpunga uwonongeka kamba ka umbombo 

Mai wina kwa Kankao kwa Chanthunya m’boma la Balaka wataya mapoto awiri odzaza ndi mpunga wophika utaonongeka kamba ka umbombo. Nkhaniyi ikuti malinga ndi chikondwelero cholowa m’chaka chatsopano kagulu ka amai ena omwe amagwira ntchito yolera ana amasiye ku malo ena m’bomalo anakonza phwando pomwenso panali zakudya zosiyana-siyana. Itakwana nthawi ya madyelero m’modzi mwa amaiwo yemwe amataka-taka pophika zakudyazo anabisana mapoto awiri a mpunga wophika-phika komanso mphika umodzi wa nyama. Koma mphuno salota anthu pa phwandolo anadya zakudyazo mpaka kuzilephera, kotero kuti zina anagawana amaiwo. Mai yemwe anabisa mapoto awiri a mpungayo komanso mphika wa ndiwo anangoti kakasi kusowa chochita ataona kuti zakudya zamuchulukira. Kamba ka izi mpunga wina womwe maiyo anabisa unafika posasa. Amai ena pa gululo anazindikira kuti m’nzawoyo ndi waumbombo zomwe sizinamuthandize.

 

Khoswe wa matsenga asowetsa ndalama

Mwamuna wina wa bizinesi ku msika wa Matabwa pa boma la Kasungu analira ngati mwana khoswe wamatsenga atasowetsa ndalama zomwe anagulitsa malonda ake pa tsikulo zokwana 120-thousand Kwacha. Watitumizira nkhaniyi wati pa tsikulo m’modzi mwa makasitomala anafika ku malowo komwe anagula matabwa a ndalama zokwana 20-thousand Kwacha. Ndipo mwamunayo atangochoka ku malowo khoswe yemwe sanadziwike komwe anachokera analumpha ndi kupana ndalama za pepala zokwana 120-thousand Kwacha zomwe mwamunayo anagulitsa pa tsikulo ndikuthawa komanso kuzimilira osaonekanso. Mwamuna wa bizinesiyo anakuwa kuitana anthu kuti amuthandize kugwira khosweyo koma sanaoneke. Mwamuna wa bizinesiyo anafika polira ngati waferedwa uku akugubuduka. Mwamuna wa bizinesiyo waopsyeza kuti aponda-ponda kuti yemwe akumuseweretsa m’matsenga aone chomwe chidameta nkhanga mpala.

 

Get Your Newsletter