Mphunzitsi wamkulu wa sukulu ya Kasitu CDSS, imene ili kudera la kumpoto m’boma la Nkhotakota, a Mixom Gama, ati ophunzira wawo Owen Nkhoma analephera kulipira ndalama ya mayeso a boma yokha a JCE yomwe ndi K19, 000.
Iwo ati sizoona kuti mnyamatayu akufunikira ndalama ya school fees, ndipo atsindika kuti iye ali pa bursary ya boma imene inayamba kumulipilira school fees kuyambira ali Form 1.
A Gama anatinso pali chiyembekezo kuti mnyamatayu abwerelanso m’kalasi m’mwezi wa September chaka chomwe chino.
Ndipo m’modzi mwa akuluakulu a khonsolo ya bomali, a McDonald Mpichi, ati aphungu akunyumba yamalamulo ndi amene amasankha ophunzira amene angapindule ndi CDF.
A Mpichi anapitiliza, “ngati ndisakulakwitsa ndalama za mayeso amayenera kulipira okha ophunzira.”
Phungu waderali, a Henry Chimunthu Banda, nawo atsindika kuti mwanayu alidi pa mndandanda wa ophunzira amene akulipiliridwa fees.
“Mwanayo akulipira fees ndi CDF. Umboni wake ndi umenewo,” a Chimunthu Banda anatero.
Dzulo, m’modzi mwa anthu achifundo, a Wesley Kalenga, anapempha akufuna kwabwino, kudzera pa MBC Digital, kuti amuthandize mnyamatayu ku nkhani ya fees.