Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani Sports

FAM ikufuna abale ambiri kumpira wa miyendo

Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo m’dziko muno la FAM lati likupanga chothekera kuti lidzikhala mu ubale wabwino ndi kampani komanso anthu ochita za malonda ndi cholinga chotukula masewerowa.

Membala wa komiti yaikulu ya FAM, Daudi Mtanthiko, wayankhula izi pabwalo la zamasewero la Nsanje pomwe komiti yoyendetsa mpira m’chigawo cha kummwera, mogwirizana ndi kampani ya Betika, amakhazikitsa mpikisano wa chaka chino wa Betika Southern Region Football Association Division One.

A Mtanthiko ati kubwera kwa kampani zothandiza masewero a mpira wa miyendo ngati Betika kuthandiza kuti masomphenya a bungwe lawo akwaniritsidwe mosavuta.

Kampani ya Betika ikuthandiza mpikisanowu ndi ndalama zokwana K27 million pachaka ndipo anapanga mgwirizano wa zaka zitatu.

Pa mwambowu, omwe unatsogoleredwa ndi wa pampando wakomiti yoyendetsa mpira chigawo cha kummwera a Raphael Humba ndi mamembala ena, kunafikanso mkulu wa kampani ya Betika m’dziko muno, a Gift Govati, ndipo timu ya Nsanje United yagonjetsa timu ya Chikwawa United ndi zigoli zitatu kwa duu.

Wolemba: Amin Mussa

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Zinthu zambiri zasintha — Chithyola Banda

Justin Mkweu

Zaka zitatu pogulitsa makala mosatsata lamulo

Mayeso Chikhadzula

Region 5 to feature new sporting codes

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.