Oyimba nyimbo za Afro, Emily ‘Emmie Deebo’ Zintambira wasainirana mgwirizano okhala kazembe wa kampani yopanga sopo ya Hirwa General Dealers wandalama zokwana K80 million.
Emmie Deebo anayamikira kampaniyi kaamba kamgwirizanowu ndipo wati achita zotheka kuti asaulutse koteratera.
Ofalitsa nkhani ku kampaniyi, a Klaus Chikufenji, ati mgwirizanowu ndi wamiyezi isanu ndi umodzi ndipo cholinga chake ndikufuna kutukula achinyamata pa luso lawo komanso nkhani zamalonda.