Anthu opyola 8,000 m’ma boma a Mulanje ndi Phalombe tsopano ali ndi madzi aukhondo kutsatira chitukuko chimene nthambi ya DoDMA yachita m’madera a Kamwendo ndi Misewufolo m’maboma awiriwa.
Ntchito yogawa madzi a m’mipopiyi, amene akuwapopa ndi mphamvu yadzuwa,ayigwira pansi pa Post Cyclone Idai and Kenneth Emergency Recovery and Resilience Project.
Wapampando wa komiti yoyendetsa chitukukochi kwa Kamwendo, a Blessings Mikeas, anati izi zithandiza kwambiri chifukwa madzi am’mijigo mderali amatuluka amchere.
M’modzi wa akuluakulu a Dodma, a Moses Chimphepo, anati zitukuko zotere zachitika m’maboma asanu ndipo anthu a mmaderawa atenge umwini wa chitukukochi kuti chikhalitse.
Kwinanso kumene DoDMA yachita chitukukochi ndi maboma a Chikwawa, Zomba ndi Nsanje.