Prezidenti wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, watsimikizira anthu a m’boma la Dowa kuti vuto la madzi likhala mbiri ya makedzana.
Poyankhula kwa khwimbi la anthu limene linasonkhana pa Madisi Trading Centre, Dr Chakwera wati kubwera kwa chitukuko cha madzi Cha Kholongo Multipurpose Dam zithandizira kwambiri kusintha miyoyo ya anthu a m’boma la Dowa ndi madela wozungulira.
Pa chifukwachi, mtsogoleri wa dziko linoyu wapempha aMalawi kuti adekhe pomwe akukhazikitsa zitukuko zosiyanasiyana mokomera aMalawi onse.
Chitukuko cha madzi cha Kholongo Multipurpose Dam chikuyembekeza kutha chaka cha mawa.