Timu ya Dedza Dynamos tsopano izidziwika kuti Premeir Bet Dedza Dynamos kutsatira m’gwirizano umene yakhazikitsa ndi kampani ya Premier Bet wa ndalama zokwana K100 million wa chaka chimodzi.
Ngati mbali imodzi yowalimbikitsa osewera a timuyi, Premier Bet idzipereka ndalama zokwana K100,000 kwa osewera bwino pa mwezi ndipo K500,000 idzipita kwa osewera bwino pa chaka.
Otsatira komanso kuchemelera timuyi ndi amene adzisankha osewerawa ndipo ndalama yokwana K200,000 idzipita kwa ochemelera amene waonetsa chikondi ku timuyi.
Olemba : Amin Mussa