Nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda ati zomwe lanena bungwe la zachuma padziko lonse la IMF kuti chuma cha dziko lino chikwera ndi 3.3 percent chaka chino, zaonetseratu kuti ndondomeko zachuma tsopano zayamba kuyenda bwino m’dziko muno.
Chaka chatha, chuma cha dziko lino, chinakwera ndi 1.6 percent.
A Chithyola-Banda ati izi zaonetseratu kuti mfundo zomwe boma linaika pothana ndi mavuto a zachuma m’dziko muno, zikubereka zipatso zabwino.
Iwo ati kukwera kwa chuma komwe bungwe la IMF lalengeza, kufikila munthu aliyense zomwe zithandize kuti aliyense awone kusintha pa moyo wake.
Akuluakulu a bungwe la IMF anali m’dziko muno kwa masiku atatu motsogozedwa ndi a Mika Saito pomwe amazakambilana ndi akuluakulu a boma.
Nthumwi za bungaeli zinaonanso momwe boma likuyendetsera dongosolo komanso mfundo zobwezeretsa chuma m’chimake kutsatira ndalama zomwe bungweli linapereka kudziko lino zothandiza kukonzanso chuma chake.
Wolemba: Arthur Chokotho ndi Blessings Kanache.