Mkulu wa zaumoyo ku Blantyre, Dr Gift Kawalazira, ati anthu enanso awiri amwalira, kufikitsa chiwerengero cha anthu omwe afa atamwa mowa umene ukudziwika ndi dzina loti ‘ambuye tengeni’ kapena magagada kwa Manase pa 7.
Iwo ati zotsatira zomwe apeza atapima limodzi lamatupi a anthu omwe amwalirawo, zasonyeza kuti anthuwa afa kamba komwa mowa omwe unasanduka wapoizoni owopsa.
Dr Kawalazira ati akuchita kafukufuku otsiriza pa thupilo ku laboratory.
Anthu asanu ndi atatu ndiwo anafika pa chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth akuonetsa zizindikiro zofanana, onse ochokera kwa Manase atamwa mowawu, ndipo asanu anamwalira pofika loweruka, ndipo awiri amwaliranso pofika lero.
Pakadali pano, munthu mmodzi ndiye akulandirabe mankhwala pachipatalachi.