Katswiri wankhonya Isaac Chilemba wagonja m’masewero ankhonya amene anachitikira munzinda wa Moscow mdziko la Russia.
Mundime yachiwiri mwandime zisanu ndi zitatu, Chilemba anagwetsedwa ndikukanika kuima atathambitsidwa ndi zibakera zochokera kwa Alexei Papin wam’dzikolo.
Papin anali atapambana nkhonya 16 ndi ma knockout 15 komanso kugonja kamodzi asanakumane ndi Chilemba.
Chilemba, yemwe analengeza kuti wasiya nkhonya miyezi yapitayo, asadalowe m’bwalo la masewerowa anati sakuopa ndi mbiri ya Papin.
Aka sikoyamba Chilemba kugonja ndi akatswiri am’dziko la Russia kaamba koti anagonjaponso ndi Dimitry Bivol katakwenso pamasewerowa.