Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera walangiza aMalawi kuti asamamvere zonena za andale ena amene akunamiza anthu pofuna kungotchuka pa ndale chabe.
A Chakwera ati andale ena akunamiza anthu kuti adakakhala kuti iwo akulamula dzikoli, mavuto ena omwe alipo panopa sakanapezeka. Dr Chakwera ati zoona zake ndi zakuti mavuto ena alipowa anadza chifukwa cha nkhondo yaku ulaya pakati pa maiko a Russia ndi Ukraine, komanso matenda a Covid 19 ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi monga Cyclone Ana komanso Gombe.
Dr Chakwera anati salola kuti anthu ena agwetse ulesi boma komanso aMalawi ndipo anati apitiliza ntchito yokonza zinthu mdziko muno.
“Tikudziwa kuti ena agundika, kulankhula zambiri komanso kunamiza aMalawi, enawo tikudziwa kuti anaba ndalama zaboma koma ife sitigwetsedwa ulesi tipitiliza kugwira ntchito zokweza dziko lino,” anatero Dr Chakwera.
Pa nkhani ya ulimi, Dr Chakwera ayamika kampani ya Philip Morris International kubwera kuno ku Malawi kudzalimbikitsa ulimi ogwiritsa ntchito zipangizo za makono monga ma tractor.
Iye walangizanso alimi kutsata njira zamakomo za ulimi zothandiza kubwezeretsa chonde mu nthaka.
Olemba: Isaac Jali