Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera akuyembekezeka kufika ku Chichiri Trade Fair Grounds komwe atsegulire chionetsero cha za malonda.
Bungwe la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) ndi lomwe likuchititsa chionetserochi, chomwe chikutsindika pa mfundo zolimbikitsa kupanga katundu woyenera kutumiza kunja kwa dziko lino.
Padakali pano, khamu la anthu lafika kale ku Chichiri komwe kuli kampani pafupifupi 177 zomwe zichite nawo zionetserozi kuyambira lero mpakana sabata yamawa, Lachitatu, pa 29 May.
Olemba: Earlene Chimoyo ndi Austin Kachipeya