Bungwe la mpingo wakatolika la Catholic Development Commission of Malawi (CADECOM) lapereka ndalama zokwana K63,150,000 ku mabanja 421 omwe akhudzidwa ndi njala kwa Mfumu yaikulu Phweremwe m’boma la Phalombe ndipo banja lililonse lalandira K150,000.
Mmodzi mwa akuluakulu a CADECOM, Vincent Tenthani, wati apereka ndalamazo kuti agule chakudya potsatira njala yomwe yadza kamba ka nyengo ya El nino komanso ngozi zachilengedwe zomwe zasokoneza ulimi m’bomalo.
A Tenthani ati apereka ndalamazo kwa anthu amene sangathe kugwira ntchito, kuphatikizapo okalamba ndi olumala.
Mmodzi mwa anthu omwe alandira nawo ndalamazo, mayi Andoleje Fulusa a zaka za mma 70, ayamikira bungweli ponena kuti tsopano akwanitsa kugula chimanga.
Ndithandizo lochokera ku bungwe la Trocaire, bungwe la CADECOM lati likufuna kufikira mabanja 891 ndi thandizo la ndalama m’bomalo.