Malawi Broadcasting Corporation
Africa Crime Environment Local News Nkhani

BWALO LA MILANDU LABWEZA GALIMOTO YA UMBONI WABOMA

Bwalo la milandu la Magistrate mu mzinda wa Blantyre la lamula a Polisi komanso gawo la boma loona za nkhalango kuti abweze galimoto ya mtundu wa Truck ya Scania, yomwe nambala yake ndi NN 10435 yomwe ili yokula ndi matani khumi.

Galimoto-yi amayisunga ku ma ofesi azakhalango kaamba kogwiritsidwa ntchito ponyamula makala, zomwe zili kuphwanya lamulo.

Apolisi adaigwira galimotoyi, kutsatira pamene anthu ena adawatsina khutu, ndipo anapeza kuti a Jonas Billiat ndi amene amayendetsa komanso ananyamula matumba a makala 205 pa roadblock ya Ngumbe pa 21 December 2023 m’mamawa mu mzinda wa Blantyre.

Malinga ndi zomwe MBC yapeza, mkulu wa polisi woona zotengera milandu kubwalo la milandu, yemwe ndi wa chiwiri kwa komishonala a Levison Mangani, anapempha bwalo-li kuti lisapereke galimotoyo pokhala kuti mwini wake ndi amene adapalamula mlanduwu ndipo kuti galimotoyo ili ngati umboni umodzi waukulu waboma.

Komabe magisitireti amene akuunguza nkhaniyi wapereka galimotoyi kwa a Biliati omwe adakali pa belo kutengera zomwe adayankhula owaimilira mlandu wawo.

Kuyambira chaka chatha apolisi mogwirizana ndi gawo la boma loona za nkhalango komanso bungwe lolimbana ndi m’chitidwe wa ziphuphu ndi katangale, akhala akugwirira limodzi ntchito yothana ndi mchitidwe wosakaza nkhalango pootcha makala.

Nkhaniyi ikuyembekezeka kulowanso kubwalo la milandu pa 8 February 2024.

Olemba: Mayeso Chikhadzula

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

BeFIT programme to improve literacy, numeracy skills

MBC Online

Ntchito ndi zambiri ku Israel koma tikufuna olimbika, latero boma la Israel

MBC Online

Malawi Hockey Team struggle in Zambezi Test Series opener

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.