Malawi Broadcasting Corporation
Local News Nkhani

Bushiri afikira anthu aku Nsanje ndi chakudya

Pomwe anthu akupitilira kuvutika ndi njala kuchigwa cha mtsinje wa Shire, Mneneri Shepherd Bushiri wapereka chimanga mdera la mfumu yaikulu Mbenje m’boma la Nsanje.

Thandizo lachakudyali lapita kwa anthu omwe ndi ovutika kwambiri, zolima zawo zinaonongeka nding’amba ndipo akhala akudya zinthu zosadziwika bwino kaamba kosowa pogwira.

A Fanuel Banda, mmodzi mwa anthu omwe alandira nawo thandizoli,  anati anataya akazi awo atagwidwa ndi ng’ona ku mtsinje komwe amakasaka zakudya zakuthengo zotchedwa nyika.

Polankhula pa sukulu ya Nyamitala komwe amagawa chimanga, a Bushiri anati ndi zosakhala bwino kuti anthu afike potaya moyo kaamba kosaka zakudya mmalo owopsa komwe kukupezekanso ng’ona.

Pamenepa iye wabwerezanso kupempha kampani, mabungwe omwe siaboma komanso anthu akufuna kwabwino kuti agwirane manja ndi boma kuthandiza anthu omwe avutika ndi njalawa, ponena kuti achuluka boma palokha silingakwanitse kufikira aliyense.

‘Iyi ndi nthawi yowawitsa, ndipo ndizomvetsa chisoni kuti anthu akuvulala ena kufa kumene kuti apeze chakudya. Komabe pali chilimbikitso kuti omwe ali nazo zochuluka akhoza kuthandizana ndi boma kuti ovutikawa apeze zakudya,” watero mneneli Bushiri.

Pakadali pano, Bushiri wagawa kale chakudya mmaboma a Ntcheu, Mulanje, Thyolo, Zomba, Lilongwe, Nkhatabay, Mzimba komanso Nsanje.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

PRISONS NOT PUNITIVE FACILITIES – ZIKHALE NG’OMA

MBC Online

VETERAN POLITICIAN MWAMBUNGU DIES

MBC Online

Shack heist gone wrong

Charles Pensulo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.