Malawi Broadcasting Corporation
Local News Nkhani

Bungwe la Red Cross lapereka ndalama kwa mabanja okhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi

Bungwe la Malawi Red Cross Society masana ano lapereka thandizo la ndalama kwa mabanja omwe anakhudzidwa ndi madzi osefukira m’boma la Nkhotakota pa msasa wa Ngala.

Banja lililonse pa mabanja okwanira 579 omwe ali pamsasawu alandira ndalama zokwanira K100,000 kuti ziwathandizire pamiyoyo yawo.

Pakali pano, mmodzi mwa akuluakulu ku nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzi ya DODMA, a Fedson Chikuse, ayamikira bungwe la Malawi Red Cross Society kaamba kathandizoli.

A Chikuse apempha anthu omwe ali ndi kuthekera kuchoka pamsasawu kuti achoke ndikukayamba moyo wina.

“Musakhale pamsasa pano kaamba kodikira thandizo lochoka kuboma kapena mabungwe popewa kuti ntchito zachitukuko m’makomo zingaimenso,” anatero a Chikuse.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Capacity building crucial for effective research recommendations — NPC

Lonjezo Msodoka

Ntchisi rolls out MEC registration

MBC Online

Private sector crucial in ending child labour – Education activist

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.