Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yati itenga nawo mbali mumpikisano wa CAF Champions League chaka chino.
Izi zikudza pamene pakhala pali mtsutso pakati pa otsatira masewero ampira wamiyendo ngati ndi koyenera kuti timuyi itenge nawo gawo mumpikisanowu kapena wa Confederation Cup.
Mmodzi mwa akuluakulu a Bullets, Albert Chigoga, wati apereka kalata zofunikira zonse zoonetsa chidwi chawo choti atenge nawo gawo mumpikisanowu chaka chino ku bungwe la Football Association of Malawi.
Chigoga wati agwiritsa ntchito ndalama zambiri mumpikisanowu ngakhale akana kunena mlingo wa ndalamazo.
Bungwe la Football Association of Malawi posachedwapa lidalengeza kuti lidzithandiza matimu omwe adzitenga nawo gawo muchikho cha CAF.